Nkhani

Boma lapereka K100biliyoni yogulira chimanga

Nduna ya za chuma, mapulani a za chuma, komanso kupereka mphamvu ku anthu a Joseph Mwanamvekha yati boma lapereka K100 biliyoni zogulira chimanga ku nthambi ya National Food Reserve Agency (NFRA).

Poyankhula m’Nyumba ya Malamulo mkati mwa sabatayi, a Mwanamvekha anati ndalamazo ndi gawo la ntchito yolimbikitsa chitetezo cha chakudya m’dziko muno pamene akatswiri akulosera za nyengo ya El Niño yomwe imapereka chiopsezo ku ntchito za ulimi.

Public expenditures remain largely focused on maize . | Nation

Malingana ndi ndunayo, cholinga cha ndalamazo n’kufulumizitsira ntchito yogula chimanga kwa alimi m’madera kuti nkhokwe za boma zikhale zodzala bwino pofuna kuteteza Amalawi ku njala yomwe ingadze kaamba ka kuchepa kwa zokolola.

“Nditsimikizire Nyumba yolemekezekayi kuti mmene ndikuyankhulamu, nthambi ya NFRA ili kale ndi chimanga m’nkhokwe zake, china chochokera ku Zambia, komanso tapereka K100 biliyoni ku nthambiyi kuti igule chimanga china choonjezera,” adatero a Mwanamvekha.

Ndunayi idatinso nthambi yoona zogula ndi kugulitsa katundu wa boma ya Public Procurement and Disposal of Assets Authority (PPDA) idapereka chilolezo ku NFRA kupitiriza ndi ntchito yogula chimanga itaunikira ndondomeko zonse zokhudza dongosololi.

Komabe, a Mwanamvekha sadafotokoze chifukwa chomwe unduna wake waperekera K100 biliyoni pomwe ndondomeko yoyendetsera chuma cha boma ya chaka cha 2026/27 idapatula K60 biliyoni yokha kuti NFRA igulire chimanga.

Mkulu wa NFRA a Bruce Munthali adauza Tamvani kuti nthambiyi yalandira kale K20 biliyoni ndipo ikuyembekezera kuyamba kulandira chimanga potsatira mapangano omwe yachita ndi ogulitsa osachepera 185.

Iwo adati K100 biliyoni yomwe NFRA yalandira ithandiza kugula matani 108 000 a chimanga pa mtengo wa K900 pa kilogalamu womwe boma lidakhazikitsa.

“PPDA idatipatsa chilolezo kuti tikhoza kupereka makontalakiti omwe timayenera kupereka ndipo ndine wokondwa kuti tapereka kale makontalakiti 185 kwa ogulitsa omwe adakwaniritsa ndondomeko,” adatero a Munthali.

Iwo adatinso kuphatikiza pa matani 62 000 omwe NFRA ili nawo kale, chimanga chomwe nthambiyi ikuyembekezera kugula chidzafikitsa mlingo wa m’nkhokwe zake pa matani pafupifupi 170 000.

Komabe, a Munthali adavomereza kuti mlingowu ukhalabe wotsika ndi matani 47 000 poyerekeza ndi mlingo wa matani 217 000 womwe ndi woyenera.

Iwo adati boma likusakasaka njira zina zopezera ndalama kuphatikiza kukambirana ndi abwenzi ake osiyanasiyana kuti chimanga choonjezera chipezeke pofuna kupewa mavuto omwe angadze kaamba ka nyengo ya El Niño.

Chitsimikizo cha ndalamazi chidabwera potsatira nkhawa ya phungu wa dera la Dedza Mphunzi a Emmanuel Mawindo atadandaula za kuchedwa kwa nthambi ya NFRA ndi kampani ya Admarc Ltd kuyamba kugula chimanga kwa alimi.

A Mawindo adachenjeza kuti kuchedwaku kwapereka mwayi kwa a malonda ena kudyera alimi masuku pa mutu, komanso kulimbikitsa mchitidwe wozembetsa chimanga kupita ku maiko oyandikana nawo a Mozambique ndi Zambia kumene akuchigulitsa pa mitengo yokwera.

Poyankhapo, nduna ya za ulimi, ulimi wa mthirira ndi chitukuko cha madzi Mayi Roza Mbilizi adati Admarc yayamba kale kugula chimanga m’madera omwe ntchito yokolola inatha msanga, koma siyidafalikire m’dziko lonse chifukwa cha vuto la ndalama zogwirira ntchito.

A Mbilizi adati Admarc idapatsidwa K60 biliyoni yogulira mbewu komanso K60 biliyoni ina yolimbikitsira ntchito zake zomwe zikuyeneranso kuthandizira ntchito yogula mpunga, nandolo, thonje ndi mbewu zina.

Padakali pano mabungwe okhudzidwa ndi za ulimi achenjeza kuti kuchedwa kwa boma kuyamba kugula chimanga kwafooketsa kale ndalama zomwe alimi amapeza, komanso chitetezo cha chakudya m’dziko.

Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi a Jacob Nyirongo adati alimi ambiri agulitsa chimanga chawo kwa amalonda chifukwa boma lidachedwa kulowa mu msika. Naye mtsogoleri wa Grain Traders Association of Malawi Mayi Grace Mijiga-Mhango adadzudzula kuchedwa kwa ntchito yogula chimanga, ponena kuti kuli n’kuthekera kuonjezera ndalama, komanso kusokoneza ntchito ya boma yokonzekera kulimbana ndi vuto la kusowa kwa chakudya.

A Mijiga-Mhango adatinso pakufunika pakhale kuunikira bwino dongosolo logulira chimanga, ponena kuti kusadziwika bwino kwa mapulani a boma kwafooketsa amalonda ena kugula chimanga kuchokera kunja kuti chionjezere chomwe chilipo m’dziko muno.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button