Njira yatsopano yotololera misonkho yautsa mapiri pa chigwa
Sitolo m’madera ambiri makamaka m’mizinda ikuluikulu zakhala zotseka mkati mwa sabatayi pomwe eni sitolozo sakugwirizana ndi njira yatsopano yotolera misonkho ya VAT yomwe nthambi ya misonkho ya MRA idakhazikitsa.
Koma Lachinayi, ochita bizinesiwa adalengeza kuti ayambanso kuchita malonda awo.

Kuyambira pa 1 May 2026, MRA idayamba kugwiritsa ntchito njira yotchedwa Electronic Invoicing System (EIS) yomwe akuti izithandiza kuti boma lizitha kulondoloza msonkho ulionse kwa ochita malonda.
Msonkhowu ndi umene munthu aliyense amadulidwa akagula katundu wa mtundu ulionse ndipo ogulitsa katunduwo amayenera kukaupereka ku MRA kuti upite ku boma ukagwire ntchito za chitukuko.
Koma pakhala pali kusamvetsetsana pakati pa ochita malonda ndi nthambi ya MRA pomwe ochita malonda ena akuganiza kuti njirayo ndi yofuna kuti azigawana phindu lawo ndi boma.
Ngakhale bungwe la ochita malonda lidayimitsa zionetsero zomwe lidakonza Lachitatu, ochita malonda mu mzinda wa Mzuzu adapitirira ndi zionetserozo.
Polankhula ndi atolankhani Lachiwiri, mkulu wa MRA a Felix Tambulasi adati n’zodabwitsa kuti ochita malondawo akukana njirayo pomwe msonkho omwe ukukambidwawo amapereka ndi ogula osati ogulitsa.
“N’zomvetsa chisoni kuti amalonda ena asankha kusamvetsetsa n’kumatseka sitolo zawo ndiponso zikumveka kuti ena akumaopseza anzawo ndi cholinga chowakakamiza kuti nawonso atseke sitolo zawo.
“Chomwetu ambiri sakumvetsa nchoti msonkho omwe ukukambidwa apawu opereka ndi Amalawi osati ochita malonda, kungoti ochita malondawo ndi njira yodutsiramo msonkhowo poti umadulidwa ku katundu ogulidwa,” adatero a Tambulasi.
Woyang’anira za malamulo ku MRA Mayi Beatrice Mwangwera adati kusatsatira njira yatsopanoyo ndi mlandu ndipo uli ndi zilango zikuluzikulu kuphatikizapo kupeleka chindapusa chosachepela K5 miliyoni.
Mlumikizi wa mabungwe omwe alipansi pa Human Rights Consultative Committee (HRCC) a Fryson Chodzi adati Amalawi akuyenera kukhala mbali ya boma pa nkhaniyi chifukwa nkhani yake n’kupulumutsa misonkho yawo.
“Amalawi adziwe kuti nthawi zonse akagula katundu kulikonse pamakhala msonkho omwe amadulidwa, msonkho umene uja umafikira m’manja mwa ogulitsa aja ndiye padapezeka kuti pali ena safuna kukapereka msonkhowo ku MRA kapena amakapereka ochepa wina n’kubisa.
“Cholinga cha njira ya EIS nchoti MRA izitsatira kuchuluka kwa katundu yemwe wamalonda ali naye, kuti wagulitsa mungati pakutha pa mwezi ndipo abweretsa msonkho wochuluka bwanji. Mwanjirayi, MRA izitha kutolera msonkho onse bwinobwino,” adatero a Chodzi.
Iwo adaunikiranso kuti MRA itamatolera msonkho umenewu moyenera, boma likhoza kuchepetsa kukongola ndalama zoyendetsera bajeti yake komanso misonkho ina yomwe amapweteka nayo ogwira ntchito ikhoza kutsika.
Mkulu wabungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula katundu la Consumers Association of Malawi (Cama) a John Kapito adati kuli bwino kuti ochita malonda agwirizane ndi njirayi n’kuyamba kuigwiritsa ntchito.



