Nkhani

Malemia amangidwa zaka 21

Bwalo la majisitileti ku Zomba lachisanu lidagamula Senior Chief Malemia kuti akakhale ku ndende zaka 21 pa mlandu wogonana ndi mtsikana wachichepere komanso kuthandizira kuchotsa mimba.

Popereka chilangocho, woweruza a Elijah Daniels, pa mlandu woyamba adapereka zaka 21 pamene mlandu wachiwiri zaka 9, zonse 30. Koma a Daniels adauza bwalolo kuti achotsera zaka 9 chifukwa bwalolo chilango chake malire ndi zaka 21.

A Malemia kukwera galimoto wopita
ku ndende. I Kondwani Nyondo

Chigamulo cha a Daniels chidatsutsa zimene woimirira mfumuyo a Patrick Debwe adapempha bwalolo pa July 17 chaka chino, kuti a Malemia awalange monga munthu, Lloyd Clement, osati ngati mfumu.

A Debwe adapempha bwalolo kuti mfumuyo ikakhale ku ndende zaka 5 pa mulandu woyambawo ndi zaka zitatu mlandu wachiwiri, zonse zaka 8 pamene mbali ya boma idapempha bwalolo kuti, mlandu woyambawo zaka 21 ndipo wachiwiriwo zaka 10.

Koma a Daniels adati zifukwa zina zimene zakulitsa chilangocho ndi udindo wawo wa ufumu chifukwa aumagwiritsa ntchito molakwika.

Iwo adapereka chitsanzo kuti, tsiku limene amakagula mankhwala ochotsera mimba, dotolo adaperekera umboni kuti a Malemia adauza dotolo kuti iwowo ndi Senior Chief Malemia osati Lloyd Clement.

A Daniels adaonjezera kuti mfumuyo idali ndi mpata wodziletsa kugonana ndi mtsikanayo koma imamugonabe ka 4 mwezi uliwonse kwa miyezi 8 mpaka adamupatsa mimba.

Malinga ndi a Daniels, mfumuyo idapanga chiganizo chochotsetsa mtsikanayo mimba ndipo zitakanika poyamba, adakapanganso kachiwiri ngakhale amadziwa kuti kuchotsa mimba ndikosayenera.

“Mtsikanayo akadakhala kuti mimbayo idachoka bwinobwino osadwala kapena mtsikanayo akadamwalira pochotsa mimbayo sizikadadziwika kuti adapereka ndi mfumuyo,” adatero iwo.

A Daniels adapitiriza kuti mfumuyo imayenera kukhala chitsanzo choteteza ana ponena kuti m’misonkhano ina mfumuyo imatha kukamba zoteteza ana pamene iwo kumbali akuchitira nkhanza ana.

“Zikalata za chigamulocho zitumizidwa ku bwalo lalikulu kukatsimikizidwa, kumene chigamulocho chikhoza kukachepetsedwa kapena kuwonjezeredwa,” adatero iwo.

Woyimirira boma pa mlanduwo a nthambi ya boma yoimilira anthu pa milandu ya Director of Public Prosecutions (DPP) a Naarai Longwe ati alemekeza chigamulo chimene bwalolo lapereka.

Ku bwalolo, kudali anthu ochepa makamaka mafumu amene adali pansi pawo ndi achibale, kusiyana ndi m’mbuyomu pamene mulandu umayamba kumabwera khamu la anthu kuphatikizapo mafumu a m’maboma ena.

A Malemia amene adamangidwa pa March 25 Chaka chino, adadzodzedwa kukhala Senior Chief Malemia pa August 11 2018.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button