National News

Miyezi 12 ku ndende kwa wotaya mwana

Bwalo la Nsanje Second Grade Magistrate, Lachiwiri lidalamula mayi wina wa zaka 27 a Stella Siliva kukagwira ukaidi kwa miyezi 12 atamupeza wolakwa pamlandu wotaya mwana zomwe n’kuchimwira gawo 234 (A) la malamulo oyendetsera milandu ya upandu m’dziko lino.

Woomora boma pa milandu a Gladston Kanyezi adauza bwalolo kuti Siliva adakwatiwa mu 2015 ndipo mwamuna wake ataona usiwa ndi umphawi wa banja lake adapita ku South Africa komwe adakasaka maganyu mu 2022.

A Kanyezi adati m’chaka cha 2025 Siliva adayamba kumva mabingu m’thupi mwake zomwe zidachititsa kuti apeze chibwenzi chozimitsira motowo.

Iwo adati atayamba kudziwana awiriwa m’chaka cha 2025 adamufumbatitsa bango pa nsalu zomwe adaona kuti zidetsa mbiri yake ndi kuthetsa banja lake ndi mwamuna wake wa ku Joni ndipo adapeza njira yofuna kuthana ndi izi.

A Kanyezi adati pa 23 July Siliva adayamba kumva ululu woti akufuna kubereka koma m’malo momapita kuchipatala iye adathamangira ku zimbudzi za sukulu ya pulaimale ya Matundu komwe adabereka yekha mwana wake pa 24 July 3 koloko mbandakucha kenako ndi kumusiya m’chimbudzicho.

Iwo adati anthu ena adamva kulira kwa khandalo ndipo adamutenga kupita naye ku chipatala chachikulu ku Nsanje komwe adamwalira tsiku linalo akulandira thandizo la mankhwala.

Ataonekera pa bwalo la mlandu iwo adavomera mlanduwu ndipo adamupeza wolakwa kaamba kovomera yekha.

M’mawu awo a Kanyezi adapempha chilango chokhwima ponena mlandu ndi waukulu komanso zochita za mayiyu zidaphetsa mwana wosalakwa.

Pomwe a Siliva adapempha chifundo ponena kuti n’kuyamba kupalamula mlandu komanso amayang’anira ana ake womwe sadanene kuti alipo angati.

Poyankhulapo asadapereke chilango chake woweruza a Haneef Ngundende adati mchitidwe wozembera wokondedwa wake munthu ndi woipa kwambiri popeza umabweretsa matenda m’nyumba.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button