Chipepeso kaye musanayambe mseu
Nzika zokhudzidwa ku Liwonde m’boma la Machinga zaopsedza kuti ziletsa kuyamba kwa ntchito yokonzanso msewu wa Liwonde-Matawale (M003) pokhapokha boma litawunikanso ndalama za chipukuta misozi zomwe likupereka kwa anthu okhudzidwa ndi ntchitoyi.
Ntchito yokonza nsewuwu, omwe ndi wa ma kilomita 47 ndi ndalama pafupifupi K101 billion zomwe zikupelekedwa ndi bank yaikulu pa dziko la pansi ya World Bank, ikuyembekedzera kuyamba posachedwapa kutsatira kukhadzikitsidwa kwa ntchitoyi ndi nduna yoona zomangamanga a Jappie Mhango sabata yatha.

Chenjezoli laperekedwa Lachinayi pambuyo pa zionetsero zamtendere zomwe zinachitika mtawuni ya Liwonde gululo lisanapereke kalata ya madandaulo ku khonsolo ya bomali ya kuchepa kwa ndalama zomwe akulandira.
Polankhula pambuyo popereka kalata ya madandauloyi, woimira gulili a Grey Mpiti anati anthu omwe akukhudzidwa ndi ntchitoyi akhala akuchita zokambirana kangapo konse ndi bungwe loona za misewu komanso unduna wa zamayendwe zokhudza momwe chipukuta misozi chikuyendera, koma madando awo sanamvedwe.
Iye anati: “Sitinapatsidwe mwayi wokwanira wofotokoza madandaulo anthu. Ntchitoyi itiwonongera katundu wathu ndi mabizinesi zomwe zimatithandiza kupeza ndalama zopititsira patsogolo moyo wathu. Tikupatsidwa chipukuta misozi cha K6 000 ndipo ena cha K8 000 yokha chomwe chili chipongwe chachikulu.”
A Mpiti adatinso anthu ambiri omwe akukhudzidwa ndi ntchitoyi amadalira ma bizinesi omwe ali m’mphepete mwa msewu ndipo akuwopa kuti ndalamazi sizingakwanire kusamukira malo ena kapena kubwezeretsa miyoyo yawo.
M’modzi mwa anthu ochita buzinesi ya malo ogona a Akimu Mussa anati adagula malo motsatira lamulo kuchokera ku khonsolo ya Machinga yomwe idamugulitsa mphepete mwa msewuwo.
“Ndili ndi kalata zondiyenereza kukhala pa malowo. Kodi momwe iwo amandigulitsira malowo samadziwa kuti ndi mphepete mwanseu? Ndiye akandipatse K8 000 yokha basi?” adafunsa motero a Mussa.
Malingana ndi a Mussa, njira yomwe yagwiritsidwa ntchito popereka chipukuta misonzi sikukwaniritsa zomwe Gawo 23 la Malamulo oyendetsera dziko komanso Gawo 46 loyendetsera ntchito yomanga misewu (Public Roads Act) lomwe limafotokodza zokhudza kulipira chipukuta misonzi mwachilungamo pamene boma likutenga katundu wa anthu pa ntchito za chitukuko.
Kudzera mkalata ya madandaulo yomwe gululi lidapereka, anthuwa adatinso panali kusiyana kwa ndalama zomwe zinaperekedwa pa katundu ndi malo a anthu okhudzidwa ndi ntchitoyo adera lina monga m’mbali ya boma la Zomba.
Iwo adatinso kuwunika kwa katundu sikudaganizire mtengo wa katundu pa msika wa masiku ano, ndalama zosamukira, kutaika kwa phindu la bizinesi, ndalama zomwe eni ake anaika pokonza katundu wawo komanso kutsika mtengo kwa ndalama ya dziko lino kuyambila pomwe ntchito ya kawuniwuni idayambira.
Mwa zomwe akufuna, anthuwa apempha boma kuti lilamule kuti ntchito ya kawuniwuni pa katundu yense yemwe akhudzidwe ndi ntchitoyi ichitikenso ndipo ntchito yokonzanso nsewuwu isayambe anthu okhuzidwa asanalandire chipukuta misonzi chonse.
Iwo ati ndiokonzeka kuchita zokambirana ndi boma, koma ati akuyembekezera kuti boma liyankha madandaulo awo mkatikati mwa masiku 21 ndipo kupanda kutero, azatseka ma ofesi a khonsolo ya Machinga.
“Takonzeka kukambirana ndi boma chifukwa cholinga chathu si kukangana. Koma ngati madandaulo athu anyalanyazidwa, tipiriza kufuna chilungamo mpaka chipezeke,” yatero kalatayo.
Polandira kalata ya madandauloyo m’malo mwa khonsolo ya Machinga, mkulu woona za ulimi Raphael Mkisi adalonjeza kuti madandaulowo akafikitsidwa kwa adindo oyenelera kuti awaganizire.
Ngakhake tidayesetsa kulankhulana ndi akuluakulu oyendetsa ntchito zomangamanga pa nkhaniyi, lamya zawo zimangoyitana kufikira pomwe timasindikiza nkhaniyi.



