Ng’ona zavuta zedi ku Nsanje
Anthu okhala m’midzi ya m’madera a T/A Katunga, Kasisi komanso Mulilima m’boma la Chikwawa ati miyoyo yawo ili pa chiopsezo pomwe ng’ona zikumatuluka m’maiwe ndi m’mitsinje n’kumakagwira ziweto ngakhalenso kukwera mipanda ya nyumba za anthu.
Zina mwa ng’onazi zikupezeka m’makhwawa momwe muli madzi odikha chabe, zina m’midzi yoyandikira mtsinje wa Shire ndipo zina m’mimtsinje ing’onoing’ono posatengera kuti muli madzi ochuluka kapena ayi.

Kuyambira pomwe madzi wosefukira anadutsa m’maderawa miyezi iwiri yapitayo nkhani za ng’ona zachuluka poyerekeza ndi zaka zonse ndipo chiopsezo chakula kwambiri.
Alimi ambiri ochokera m’midzi yoyandikira mtsinje wa Shire komanso omwe amalima minda yomwe ili m’dera la T/A Kasisi anganiza zongobwereketsa minda yawo poopa kukumana ndi ng’ona akamaoloka mtsinje wa Likhubula omwe kwa nthawi yoyamba kwa zaka zochuluka sizinachitikepo.
A Nelson Chambuluka a mwa gulupu Chadula m’dera la T/A Mulilima ati: “Tili ndi mantha a boma atimangire mlatho chifukwa timadalira njira yomweyi tikamapita kolima. Apa bola tingobwereketsa anthu azitipatsa ndalama.”
Mayi Maria Pinto a m’dera lomweli nawo ati ali ndi mantha aakulu poti ngati mai amakalimanso mbali yomweyi pooloka mtsinjewu ndipo amayi ena oyembekezera amadaliranso njira yomweyi.
Iwo ati kupezeka kwa ng’ona mu mtsinjewu ndi chiopsezo ndi chipsinjo chachikulu choncho anagwirizana ndi ganizo la bambo Chambuluka loti pa mtsinjewu a boma amangepo mlatho.
Nawo T/A Kasisi ati ngati kholo ndi wokhudzika kwambiri kaamba koti anthu awo ali kakasi kuti achita bwanji kutsatira mantha omwe ali nawo choncho nkhani ya kupezeka kwa ng’ona m’malo osayembezeka monga m’makhwawa ndi m’mitsinje momwe muli madzi wochepa ngati Likhubula n’zofunika thandizo la changu kuti anthuwa akhale otetezeka.
“Nkhani yopempha mlatho pa mtsinje wa Likhubula sitinayambe lero. Pempholi litamveka msanga zikhala bwino chifukwa anthu akuvutika ena akuvulazidwa. Izi ndi zowawa kwa ine ngati kholo,”atero iwo.
Ena mwa anthuwa ati akunkhumba zongosamukira m’madera ena akutali pomwe enanso akukhululupilira kuti ng’onazi n’zamatsenga ndipo eni ake alipo ndipo si alendo koma nzika za m’midzi za m’maderawa
Lachisanu lapitalo ng’ona ina idapezeka italowa m’mudzi wa Sadulo kuchokera pa dziwe la Nachikwale lomwe lili mkati komanso moyandikana ndi msika wa Dyeratu ndipo adaipha pomwe imayesera kukwera mpanda wina kuti ilowe ndi kukapeza chakudya.
Gulupu Sadulo wa m’dera la T/A Katunga ndi ndi mmodzi mwa mafumu omwe adachita umboni ataona izi ndi maso, potengera kuti dziwe la Nachikwale lili pafupi ndi nyumba yawo.
“Ndi zoona kuti ng’ona inaphedwa pomwe imafuna kukalowa ku mpanda wina. Koma tiyamika Chauta chifukwa palibe wagwidwa ndi chirombochi,’’ adatero a Sadulo.
A Chipiliro Biliati a mwa gulupu Nyozelera, m’dera la T/A Kasisi adatinso ziweto monga mbuzi zikumadyedwa ndi ng’ona zomwe zikumatuluka pa khwawa la Chomoto ndipo zikumachita chothamangitsa ziwetozo n’kudzigwira ulendo wa m’madzi kokakhwasula.
“Pano ndiye zafika povutitsitsa, zofunika akuluakulu oona za nyama za kuthengo adzadziphe basi chifukwa zikutithera ziweto kuno” adatero a Biliati.
Bambo wa zaka 34 wochokera mwa gulupu Kajala, T/A Kasisi m’boma la Chikwawa ali pa ululu pa chipatala cha Gulupu mu mzinda wa Blantyre ng’ona itaswa mafupa ake a ku mwendo pomwe amaoloka mtsinje wa Likhubula.
Malingana ndi mbale wa a George Majamanda, a Mika amaolotsa zida zoyimbira zomwe amapita nazo ku tchalichi china kuti akagwiritse ntchito pa mwambo wa mapemphero madzulo.
Apa ng’ona idamupana mwendo ndipo adakuwa mpaka anthu ena oyandikira midzi ina pa Domasi adathamanga ndi kukamupulumutsa koma pa nthawiyi ng’onayo idali itaswa fupa la mwendo wake.
A chipatala chachikulu cha Chikwawa atalandira wovulalayu adamutumiza ku Gulupu komwe akulandirabe thandizo.
Izi zadzetsa mantha ndi mafunso ochuluka pakati pa anthu a midzi yozungulira potengera kuti aka mkoyamba kuti mtsinjewu upezeke ndi ng’ona ndipo madzi ake ngochepa.
Ngakhale izi zili chomwechi, mkulu woona za chisamaliro cha nyama za kutchire ndi chilengedwe a Brighton Kumchedwa sadayankhulepo.
Nawo unduna woona za chitukuko ndo maboma a ng’ono amapepha kuti tiapatse nthawi.



