Amanga a Chikomeni pa za chamba
Apolisi a kwa Jenda ku Mzimba Lachisanu adamanga a Ras David Chikomeni Chirwa, a zaka 49 powaganizira kuti adapezeka ndi makilogalamu 19.2 a chamba popanda chilolezo.
Iwowa ndi mmodzi mwa akuluakulu amene ali mu board yoyendetsa nthambi ya boma yoyang’anira ulimi wa chamba chovomerezeka chimene si chozunguza bongo ya Cannabis Regulatory Authority (CRA).

Iwo adamangidwa limodzi ndi a Storm Kandodo a zaka 45 wochokera m’mudzi mwa Mpulula kwa T/A Nsamala ku Balaka pa mlanduwo.
Malinga ndi mneneri wa polisi ya Jenda a Gladwell Simwaka, awiriwo adagwidwa usiku wa August 6, 2026 pa Jenda Roadblock. Iwo adati apolisi omwe ankayang’anira malowo adaimitsa galimoto ya Toyota Sienta, nambala yake BW2336 yomwe inkachokera ku Lilongwe kupita ku Mzuzu.
A Simwaka adati: “Tidapeza chamba chopanda zikalata zovomerezeka m’galimotoyo.”
Iwo adaonjeza kuti chambacho chikukayezedwa ndi boma.
A Chikomeni akhala akuchita nawo ndale pomwe ayeserapo kuima pa mpando wa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino. Koma kaamba ka kusowa kwa ndalama zokwanira, iwo akhala akulephera kupezeka pa baloti.
A Chirwa amachokera m’mudzi wa Chitichi, T/A Mzikubola ku Mzimba, pamene a Kandodo amachokera ku mudzi wa Mpulula, T/A Nsamala ku Balaka.



