A Mtsiro aiphula
Maumboni oyamikira a Ledson Mtsiro akuyenda ngati madzi m’masamba a mchezo pamene Amalawi 423 adasonkha pafupifupi K6.1 miliyoni powathokoza pa ntchito ya chitetezo imene amagwira Pa Game mu mzinda wa Lilongwe.
Ndipo anthu ena a kufuna kwabwino awapatsa a Mtsiro mapuloti awiri ndipo gawo lina la ndalamazo agulira njinga ya moto komanso laputopu ya mwana wawo Mphatso amene akuphunzira ku Mzuzu Technical College ndi kumulipirira semesita imodzi.

Ndipo kampani ya Eris Properties Malawi Li,ited, imene imayendetsa Pa Game Complex yawapatsa K300 000 kuti akagulire katundu amene akufuna, chomwechonso kampani imene a Mtsilo amagwira ntchito ya G4S yawapatsa K500 000 yokagulira katundu.
Anthuwa adasonkha ndalamazi pa chilinganizo cha Tabwera Appreciation Initiative ndipo kuyambira mwezi watha akhala akuponya limodzilimodzi malinga ndi m’thumba mwawo.
Makanema a a Mtsiro akhala akuyenda m’masamba a mchezo ndipo anthu akhala akuponya limodzilimodzi kwa a Lameck Luhanga, omwe ndi wojambula kanema ndi zithunzi ndipo ali ndi kampani ya Moving Minds Multimedia. Iwo ndi amene amajambula makanemawo.
Anthu ambiri amene akulankhulapo akuti a Mtsiro ndi wolimbikira pa ntchito, aulemu, safooka pothandiza ena poongolera malo oimika galimoto zawo, kuongolera osokera ngakhalenso kupereka chitetezo chenichenicho.
“Ndidawadziwa iwowa mmbuyomu chifukwa malinga ndi ntchito yanga, malo osavuta kukumana ndi makasitomala anga ndi Pa Game. Amandipatsa chidwi momwe amagwirira ntchito yawo n’chifukwa ndidaganiza zowathokoza,” adatero a Luhanga.
Iwo adati pomwe amayamba mwezi watha, ganizo lidali loti apeze K500 000 koma adangokwanitsa kupeza K300 000 ndipo kampani zina zidawauza kuti apereka ndalama yotsalirayo. Koma kenako chidwi cha anthu chidapitirira mpaka kufika pa K6.1 miliyoni.
“Anthu akupereka maumboni odabwitsa. Pali mkulu wina amene adaiwala zenela la galimoto losatseka. Ataona izi, a Mtsiro adaima pa galimoto pomwepo ndipo sadachoke ngakhale nthawi yake yoweruka idali itakwana. Munthu adafuna kulira atapeza kuti katundu yense ali momwemo. Ndi munthu wolimbikira,” adatero a Luhanga.
Maumboni ambiri akuperekedwa pomwe ena akuti adaona a Mtsiro akusakasaka makolo a mwana wa chimwenye amene adapezeka ali yekhayekha pa malowa mpaka kuwapeza. Ena akuti adawathandiza kuyenda ndi mbale wawo amene amalephera kuyenda mpaka kukafika malo okwerera basi.
“Zikomo chifukwa chowagwira dzanja. Ndimakumbukira tsiku lina tinkadutsa pa malowa ndi mlongo wanga amene ankadwala. Atatithandiza kuyenda naye mpaka kukakwera galimoto za chipatala cha KCH. Mpaka lero ndikakumana nawo pa malowa amandifunsa kuti achemwali ali bwanji,” adatero a Mtipe Banda.
Ndipo a Graciano Solomon adati: “Mkulu uyu amagwira ntchito. Tsiku lina ndidachita chidwi momwe amagwirira ntchito. Kunkatentha osati masewera ndipo ndidawagulira madzi kumwa.”
A Mtsiro, omwe ali ndi ana 4, Lachinayi adati athandizapo anthu ambiri koma tsiku limene amalikumbukira kwambiri ndi lomwe adapulumutsa galimoto ina imene munthu wina ankafuna kuba.
“Mudali mu 2015 pomwe amayi awiri adabwera ndi galimoto yawo koma atalowa m’sitolo, mkulu wina ankafuna kuba galimotolo. Ndidachita zonse zotheka kuteteza mpaka tidagwira munthuyo mpaka apolisi adabwera. Tsiku ilo n’kadafa,” adatero m’Khristu wa mpingo wa Chitimbe CCAP-yo.
A Mtsiro, omwe amachokera m’mudzi mwa Chitsuka kwa T/A Kayembe ku Dowa, amakhala kwa Mtsiriza ndipo adati khumbo lawo pomwe ankaphunzira sukulu. Iwo adati tsiku lina asilikali amalemba anthu ntchito pa Dowa Community Ground ndipo atapita kukayesa mwayi adapambana ndipo ulendo wa ku sukulu ya asilikali ya Mafco ku Salima.
Polankhula nawo, a Mtsiro, omwe amakhala kwa Mtsiriza mu mzindawo, adati lidali khumbo lawo kudzakhala msilikali koma zidakanika atatengedwa kale.
Iwo adati: “Asilikali adafika pa Dowa Community Ground kulemba ofuna ntchito. Adanditenga mpaka ulendo wa ku Mafco. Koma bamboo anga adanditsatira uko chifukwa nthawiyo ndidali Fomu 4 pa Chimbalu CDSS. Sindifuna ndizikamba kwambiri zimenezi kuti mzimu wa bamboo anga uziusa mu mtendere.”
A Mtsiro ndi bambo wa ana anayi: Mphatso yemwe amaphunzira ku Mzuzu Technical College komanso Stella, Lesson ndi Paul omwe adakali ku pulaimale. Iwo adati amachilimika pa ntchito yawo yomwe adayamba mu 2003 polingalira za anawa.
“Munthu umachita chimene uli. Ndimagwira ntchito yanga momwe kampani yathu imafunira. Sindingalole kuti ana anga asafale pakhomo chifukwa ndachotsedwa ntchito,” adatero iwo.



