Nkhani

Umboni wa ngozi uvuta

Komiti yomwe ikufufuza ngozi ya ndege yomwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ndi anthu ena 8 pa 10 June 2024 yamva umboni osiyanasiyana koma mkati mwa sabatayi mwatuluka umboni wogonthetsa m’makutu kuchokera kwa mboni zomwe zikuti zidali pa malo a ngoziyo ikuchitika.

Lachinayi, membala wachitetezo cha m’mudzi ku dera lomwe ndegeyo idagwera a Colrerd Nkosi omwe adafokoza za ndegeyo tsiku lomwe idachitika adauza komitiyo kuti asilikali ndi magulu ena omwe ankasakasaka ndegeyo akadawamvera, ndengeyo ikadapezeka tsiku lomwelo koma akuluakulu omwe ankatsogolera kafukufuku wa ndegeyo amakakamira mbali ina yosemphana ndi komwe iwo amawawuza kuti kwagwera ndegeyo.

“Pa mapeto pa zonse ndegeyo itapezeka, matupi ena adali panja koma ena adatsakamira mkati ndipo akuluakuluwo adayang’ana zida nkuyamba kuphwasula ndegeyo n’kutulutsamo pafupi enawo. Koma ndikuona kuti ndale ndizo zidachititsa kuti ndegeyo achedwe kuipeza komanso kuti matupiwo apezeke,” adatero a Nkosi.

Poyambirira, a Nkosi adauza komitiyo kuti adaona ndegeyo ali m’dimba lawo ikuyennda mwa pendapenda komanso ikupanga phokoso lalikulu mmawa wa pa 10 June 2024 kenako sadayionenso kenako masana adaona m’masamba a mchezo kuti ndege yomwe idanyamula wachiwiri kwa pulezidenti ndi anthu ena yasowa.

Koma a Nkosi adakwiyitsa komitiyo atanena kuti mkatikati mwa chipinda momwe amapelekera umboni wawo mudali ena owafunira zabwino komanso mudali ena omwe sakuwafunira zabwino zomwe zidapangitsa kuti wapambando wa komitiyo a Walter Nyamirandu awauze kuti aphule mawu awowo.

A Nkosi adalankhula izi ali mkatikati moyankha mvumbi wa mafunso omwe amachokera kwa phungu wa Dedza (MCP) omwe amafunsitsitsa a Nkosi ngati munthu yemwe adali pomwepo ndege itapezeka ngati amaopsezedwa pa malopo.

Naye phungu wa pakati ku Mwanza a Felix Njawala (UTM) adathambitsa a Nkosi ndi mafunso okhudza anthu omwe iwo adalankhula nawo kuwadziwitsa za ngozi ya ndegeyo koma ngakhale adakakamira, a Nkosi adanenetsa kuti sangakumbukile maina a anthu onse.

Potseka zonse, a Nyamirandu adatsimikizira a Nkosi kuti asakhale ndi nkhawa iliyonse pa za chitetezo chawo komanso kuti azikhala okonzeka kuti nthawi iliyonse yomwe angafunikenso ku komitiyo adzaitanidwanso.

Lachiwiri, a Ephraim Duma wochokera ku Lilongwe adauza komitiyo kuti patsikulo akuchokera ku Mzimba kogula njinga adaona ndegeyo itaima m’malere ndipo a Chilima adaima pa khomo akufuula kufuna thandizo koma adakokeredwanso mkati.

A Duma adati ndegeyo idanyamukanso n’kulowera m’mapiri ndipo iwo ndi anthu ena awiri adaitsatira pomwe adakapeza asilikali a nkhondo ochokera m’dziko lina akuidikilira kenako anthu ena awiri adatuluka m’ndegeyo.

“Asilikali a chilendo aja adatithamangitsa, adawomba mfuti n’kupha munthu mmodzi pomwe ineyo adandiombera katatu ku msana koma ndidapulumuka chifukwa ndine okhwima, Chipolopolo kapena chida chilichonse sizingandivulaze,” adatero a Duma.

Koma mokayikira umboniwo, phungu wa Lilongwe a Mphatso Boti (MCP), omwe adakhalako msilikali wa nkhondo ndipo ndi membala wa komitiyo adatsutsa kuti ndege ya mtunduwo siyingaime m’malere.

Koma atafunsidwa kuti zidatheka bwanji kuwomberedwa katatu osafa iwo adati,”Ndidakhwima chifukwa nthawi inayake ankafuna kundidzodza ufumu wa a Kabunduli koma zidalephereka”.

Apa, membala winanso wakomitiyo a Joshua Malango adaseleula kuti atsutse galu powawombera a Duma kuti awone ngati alidi okhwima zomwe a Duma adavomera koma wapampando wa komitiyo a Walter Nyamirandu adaseleulanso kuti mwina mankhwala a Duma adasuluka ndipo akhoza kufa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button