Amalizitsa ntchito yosamutsa Amalawi ku Joni
Gulu lomwe lakhala likuthandiza anthu omwe adathawa m’nyumba zawo ndipo amakhala movutika kutsatira zipolowe zothotha anthu a maiko ena m’dziko la South Africa (SA) lati latsiriza ntchitoyo.
Mwa zina, gululi lakhala likupereka thandizo monga chakudya komanso mayendedwe kwa anthuwa kwa miyezi inayi.

Gulu lomaliza la anthu 43 lidafika m’dziko muno usiku wa dzulo Lachitatu kuchokera ku Johannesburg.
Malingana ndi mtsogoleri wa gululo, a Stanley Onjezani Kenani, ndalama zomwe adatolera zidali pafupifupi K141.4 miliyoni.
Apa a Kenani, ayamikira Amalawi, mabungwe komanso makampani kaamba koonetsa mtima wa chikondi pothandiza anthuwa kuti abwere kumudzi.
Iwo adatinso pafupifupi K2.1 miliyoni yomwe idatsala aigwiritsa ntchito kugula mankhwala a pa chipatala cha Vibangalala Rural Health Centre, m’boma la Mzimba.
“Posafuna kubweretsa chikaiko mwa anthu, tigawa malisiti ndi umboni wa momwe timatumizira,” adatero iwo.
Mkulu wa bungwe la Malawi Diaspora Humanitarian Support Initiative mayi Zainab Kandaya Kautsi adati iyi idali ntchito yapadera yomwe imafunikira mgwirizano.
“Chisangalalo chathu sichinagone pa ndalama zomwe zidagwiritsidwa ntchito ayi, koma kuti Amalawi anzathu omwe adataya chuma chawo abwerera ku mudzi ndi ulemu,” adatero iwo.
Iwo atsindika za kufunika kopeza njira zomwe zingapititse patsogolo ntchito za chuma komanso kuteteza nzika za dziko lino zomwe zikugwira ntchito m’maiko ena kuphatikizapo South Africa ponena kuti nkhani ya Amalawi kupita kukasaka ntchito ku maiko ena ikadapitirira.



