Akufuna kumanga nyumba zoteteza ofuna kudzipha
Bungwe la Azibambo Tibe Khonde Mental Health Initiative lati likufuna kukhala ndi malo 14 m’dziko la Malawi kumene anthu angakatule nkhawa zawo pomwe malingaliro odzipha akuyala nthenje m’mitu yawo.
Mkulu wa bungwelo a Jefferson Milanzi ndiwo anena izi lero pamene dziko la Malawi lili limodzi ndi maiko onse a dziko la pansi polingalira zokumbutsa kuti kudzipha si yankho la mavuto amene tikukumana nawo.

Iwo ati chaka chino chokha akumana ndi anthu 53, amene amafuna kudzipha ndipo adawadekhetsa.
“Amakhala ndi mavuto osiyanasiyana ndipo akuchokera kosiyanasiyananso. Abambo, amayi ndi achinyamata. Tsono tikufuna tiziwafikira m’madera mwawo mogwirizana ndi apolisi komanso a za umoyo amene tikugwira nawo ntchito,” atero a Milanzi polankhula ndi olemba nkhani ku Zingwangwa Youth Centre mu mzinda wa Blantyre.
Iwo ati pofuna kumanga nyumbazi, ali ndi mgonero ku Golden Peacock Hotel mu mzinda wa Blantyre pa 3 October.
“Tikufuna kukhazikitsa malo amene anthu amene alibe Mwayi wokumana nafe pa foni azitipeza m’maderamu. Pomwe tinkayamba, tidali ku Blantyre kokha koma takhala ndi zochitika m’maboma ena monga Mzimba, Mangochi, Mulanje ndi Nsanje ndipo tikufuna kufalikira dziko.
Mwa amene takumana nawo, zikuonetsa kuti aliyense akhoza kukhala ndi chipsinjo cholingalira zodzipha,” atero a Milanzi.
Mwezi wa September udakhazikitsidwa kukhala wofalitsa uthenga woti anthu asamadziphe.



