Ndalama za CDF sizinafike ku makhonsolo
Pomwe boma lakwera pa chulu kuti lapereka K85.5 biliyoni ya CDF ku makhonsolo, bungwe loona momwe makhonsolowo akuyendera makamaka pa zitukuko la Malga lati ndalamazo sizidafike ku makhonsolo.
Izi zikuchitika pomwe kwatsala miyezi 6 kuti chaka cha bajeti ya 2026/27 chithe pomwe kutengera ndondomeko zatsopano zoyendetsera ndalama za CDF, ndalama zotsala zimayenera kubwerera ku boma.

K85.5 biliyoni yomwe mlembi woyendetsa za mphamvu ku anthu mu unduna wa za chuma a Peterson Ponderani alengeza kuti zaperekedwa kuphatikizapo K2.86 biliyoni yotukulira masewero ndi za luso, K17.18 biliyoni ya za maphunziro, K15 biliyoni ya ngongole za achinyamata komanso K18.84 biliyoni ya zitukuko zomwe zidaperekedwa mmbuyomo ndi gawo la K1.145 triliyoni yomwe ikuyenera kuperekedwa m’madera a aphungu 229.
“K85.5 biliyoni imeneyi idaperekedwa ku maboma 30 mwa maboma 36. Maboma 6 omwe sadapatsidwewo sadamalize ndondomeko zopezera makontilakitala a zitukuko za m’makhonsolo ndipo akadzakwaniritsa, adzapatsidwa,” atero a Ponderani.
Makhonsolo omwe alephera kukwaniritsa ndondomekozo ndipo sadalandile ndalamazo ndi mzinda wa Blantyre, boma la Blantyre, Chikwawa, manisipalite ya Kasungu, Mulanje ndi Nsanje.
Koma mkulu wabungwe la Malga a Hadrod Mkandawire ati ndalamazo sizidafike m’mabuku a makhonsolo, kutanthauza kuti zitukuko zikadali m’mazira.
“Makhonsolo angolandira chidziwitso kuti ndalama zatuluka koma ndalamazo sizidafike m’mabuku a ku banki,” adatero a iwo.
Wapampando wa komiti yoona za maboma aang’ono ku Nyumba ya Malamulo a Edward Chileka Banda adayamikira kutuluka kwa ndalamazo koma adapeleka nkhawa yoti sizikutanthauza kuti ndalamazo zafika ku makhonsolo.
“Ndi nkhani ina kutulutsa ndalama ku thumba la boma ndipo ndi nkhani inanso kutumiza ndalamazo komwe zikuyenera kupita. Komabe Nyumba ya Malamulo ikhala ikulondoloza zonse,” adatero a Chileka Banda.
Iwo adatinso anthu eni ndalama za CDF m’makhonsolo azilondoloza kuti kodi alandirako ndalama zingati mwa ndalama zonse za CDF zomwe akuyenera kulandira.
Mkulu wa bungwe loona kuti zinthu zikuyenda m’chilungamo la Centre for Social Accountability and Transparency a Willy Kambwandira ati akuluakulu a m’makhonsolo omwe sadalandire ndalama zawo adziwe kuti akupweteketsa anthu awo.
“Komanso pali mafunso kuti kodi chifukwa chomwe chaperekedwa choti makhonsolo enawo sadamalize ndondomeko zopezera makontirakitala n’chomveka kapena ndalama zangochepa m’boma,” adatero a Kambwandira.
Koma wapampando wa bungwe la Malga a Jomo Osman adatsimikiza kuti maboma 6 omwe asiidwawo sadakwanitse ndondomeko zomwe zimafunikira ndiye boma limaopa kuphwanya ndondomeko zake zomwe.
Pomwe akadaulo ena ati bajeti ndi kupanga zinthu poyera ndiwo mavuto akuluakulu.



