Mkokemkoke pa za maufumu
Pali mkokemkoke pakati pa maufumu a m’dziko lino ndi boma pa malire amene mbali ziwirizi zingatenge potsatira malamulo.
Chikalata chimene adasaina mlembi wamkulu wa unduna woona za maboma aang’ono mbusa Moses Chimphepo adalemba pa 7 September. Iwo adati malamulo salola kuti m’dziko muno mukhale maufumu, kingdom m’Chingerezi, ndipo pasakhale wina wotchedwa mfumu ya mtundu.

“Malamulo okhudza maufumu salola kuti pakhale ufumu m’Malawi muno. Mafumu ntchito yawo n’kulimbikitsa chikhalidwe ndipo timalemekeza ntchito yaikulu imene amagwira mbali imeneyo komanso pa nkhani ya chitukuko,” adatero a Chimphepo.
Koma tsiku lotsatira, a Mzimba Heritage Association, omwe amaimirira ufumu wa Inkosi ya Makhosi M’mbelwa V, yemwe ndi mtsogoleri wa Angoni a Zwangendaba Jele limodzi ndi a Maseko Ngoni Heritage Trust omwe amaimirira ufumu wa Inkosi ya Makhosi Gomani V, adatulutsa chikalata chawo momwe adati maufumu oteteza chikhalidwewa sakukhulana konse ndi boma, ndipo sapereka chiopsezo chilichonse ku mgwirizano wa anthu m’dziko.
Chikalatacho, chimene adasaina ndi alembi a mabungwewo a Khumbo Bonzoe Soko komanso Impi Kandi Padambo, chidatsindika kuti maufumuwa ayenera kunyadiridwa.
Iwo adatsindika kuti pomwe boma la atsamunda lidakhazikitsa Nyasaland Districts Protectorate pakati pa 1891 ndi 1893, Angoni a Maseko adakhazikitsa ufumu wawo kumwera ndi pakati pa dziko lino m’zaka za m’ma 1867 mpaka 1870 pansi pa Chidyaonga ndi iNkosi Tshikusi.
“M’maiko ena a mu Africa maufumu amakhala bwinobwino ndi boma ndipo amawalemekeza. Mwachitsanzo, ku South Africa kuli ufumu wa Zulu motsogozedwa ndi Mfumu Misuzulu kaZwelithini m’malamulo aakulu a dzikolo. Nako ku Uganda kuli ufumu wa Buganda motsogozedwa ndi Kabaka Ronald Muwenda Mutebi II. Nako ku Ghana kuli ufumu wa Ashanti motsogozedwa ndi Otumfuo Nana Osei Tutu.
Ndipo poyankhapo pa tsamba lawo la mchezo la Facebook, Kalonga Sosola IX ya Achewa adavomereza kuti maufumu ndi akale kuposa boma la Malawi. Iwo adati palibe umboni kuti ngakhale boma la atsamunda lidathetsa maufumu.
“Zolankhula zathu [ndi maufumu Achingoni] ndi zimodzi tangosiyana zaka zomwe tidafikira kuno ku Malawi. Ndipo dzina la Malawi likuchoka pa Maravi Kingdom ndiye kuundira [kukwirira] mbiri yathu kutivuta chifukwa ana athu adzasowa poloza a ku unduna wa maboma aang’ono akadzapuma pa ntchito yawo,” adatero iwo.
Ndipo adaonjeza kuti akambirana ndi mitundu ina kuti aitanitse mkumano ndi boma kuti dziko la Malawi likhale la bata ndi mtendere.



