‘Chikondi chizidutsa malire’
Chikondi chomwe chidayambira pa tsamba la pa Intaneti lofunafuna zibwenzi chasintha kukhala banja kwa mayi wa malonda a ku Malawi, Jacqueline Msiska Bokosi, ndi nzika ya ku United States of America (USA), Ken Kilmer, kusonyeza kuti chikondi chimatha kugonjetsa mtunda komanso kusiyana kwa zikhalidwe.
Awiriwa adakumana mu September chaka chatha pamene mnzake wa Bokosi adamulimbikitsa kulembetsa pa tsamba la Match Dating. Kumeneko ndiko adakumana ndi Kilmer, yemwe ndi nzika ya ku USA yobadwira ku San Diego, m’boma la California.

Atadziwana kudzera pa Intaneti, adasinthana manambala a foni ndipo awiriwo adzachezerana ku America, maso ndi maso. Apo ubwenzi wawo udasintha n’kukhala chikondi.
Komatu ulendo wawo siudakhale wophweka chifukwa zikhalidwe zawo n’zosiyana, nthawi zina ankamamvetsetsana molakwika, zomwe zidachititsa kuti ubwenzi wawo usamayende.
“Chimodzi mwa zovuta zazikulu ndidaphunzira pomwe ndidapita ku America chidali choti ndizolowera moyo ndi chikhalidwe chosiyana ndi chimene ndidakulira nacho,” adatero iye.
Ndipo adaonjeza kuti m’mabanja ambiri a ku Africa, amayi amayembekezeka kukhala ndi udindo waukulu wosamalira ntchito za pa khomo.
Koma kwa Kilmer, ntchito za pa khomo ziyenera kugawidwa mofanana pakati pa mwamuna ndi mkazi. Chifukwa cha kusiyana kumeneku, Kilmer poyamba ankaganiza kuti Bokosi ankachita ntchito za pakhomo chifukwa chofuna ndalama zake, zomwe zidayambitsa kusamvana pakati pawo.
Ngakhale panali mavutowa, awiriwa adasankha kukambirana m’malo molekana. Atakhala pansi n’kukambirana momasuka, adapeza njira yothetsera kusiyana kwa zikhalidwe zawo.
Bokosi adati ubwenzi wawo udayambanso kuyenda bwino pa February 14 chaka chino, tsiku limene dziko lonse linkakondwerera tsiku la Valentine.
Chikondi chawo chidakwaniritsidwa pa July 31 pamene adakwatirana pa mwambo wa boma womwe unachitikira ku Bothell Courthouse ku Bothell, ku Washington m’dziko la USA.
Kilmer, yemwe ali ndi zaka 53, ndi woyamba kubadwa m’banja la ana 9 ndipo amagwira ntchito ngati wachiwiri woyamba wa Pulezident wa kampani ya Wealth Management pomwe Bokosi ali ndi zaka 40, ndipo ndi mwana wachitatu m’banja la ana 7. Iye ndi mwini wa CTS Courier, CTS Funeral Services komanso CTS Spare Parts.
Pochokera pa zomwe adakumana nazo, awiriwa akulangiza achinyamata ndi mabanja atsopano kuti aziika Mulungu patsogolo pa moyo wawo komanso kugwira ntchito molimbikira pa chilichonse chimene amachita.



