Nkhani

Apempha a Chaponda kuganizira Amalawi

Atatengetsa boma pa nkhani yokhudza lipoti la ngozi ya ndege Lachiwiri m’Nyumba ya Malamulo, mtsogoleri wa otsutsa boma m’nyumbayo a George Chaponda adatsogoleranso aphungu a chipani cha DPP kunyanyala zokambirana Lachitatu.

Izi zidachitika mmasiku awo oyambirira kutsogolera mbali yotsutsa boma m’nyumbayo atatenga udindowo kuchoka kwa a Kondwani Nankhumwa omwe adatuluka m’chipani cha DPP n’kukayambitsa chipani chawo cha PDP.

Chaponda

Malingana ndi a Chaponda, chipani chawo cha DPP sichikugwirizana ndi ganizo lokweza mafuta a galimoto nkhani yomwe nyumbayo inkakambirana pomwe iwo ndi aphungu a DPP adatuluka kuti asakambirane nawo.

“Ife sitikugwirizana nazo zokweza mafuta a galimoto chifukwa zimenezi zipweteka Amalawi kwambiri. Mafuta a galimoto akakwera, mitengo ya katundu wambiri imakweranso ndiye ovutika sitikhala ifeyo opanga ziganizo koma Amalawi n’chifukwa chake ife tatuluka,” adatero a Chaponda.

Kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa ngati a Chaponda ayamba ntchito yawo yotsogolera mbali yotsutsa boma, iwo adati chinsinsi chagona poika moyo wa Amalawi pa mtima osatsogoza ndale.

Iwo ati andale ambiri amlephera ntchito yawo kaamba koti amatsogoza tsogolo lawo pandalezo kuyiwala anthu omwe akuwayimilira ndipo potero iwo amawona ngati akukhoza osadziwa kuti akupotoza.

“Chinsinsi chachikulu n’kuika moyo wa anthu pa mtima, ndale zizibwera pambuyo. Chomwe chimachitika nchakuti andale ambiri amatsogoza ndale zinazo n’kumabwera pambuyo pake pomwe siziyenera kukhala choncho,” atero a Thindwa.

Iwo adapereka chitsanzo cha chifukwa chomwe a Chaponda adatsogolelera aphungu a DPP kunyanyala zokambirana kuti sakugwirizana ndi ganizo la kukwera kwa mafuta a galimoto ponena kuti akadayamba amvetsetsa kuti ganizolo labwera bwanji.

“Ngakhale kuwafunsa a bungwe loyang’anira za mphamvu za magetsi ndi mafuta a galimoto la Mera, akuuzani kuti boma likugula mafuta pa mtengo wokwera kuposa ndalama zomwe likupeza. Izizi zikungotanthauza kuti mtsogolomu boma litha kudzakhala lopanda ndalama zogulira mafuta,” atero a Tindwa.

Iwo ati magulu onse omwe akuvomereza kuti mtengo wa mafuta ukuyenera kukwera akulingalira ataona za mtsogolo kuti akapanda kuchitapo kanthu monga kukweza mtengo wa mafuta, mtsogolo muno dziko la Malawi lidzakhala lopanda mafuta agalimoto.

Wapampando wa komiti yomwe imayang’anira za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo yomwenso imakhudza nkhani za mafuta a galimoto a Welani Chilenga adati padakalipano makampani oitanitsa mafuta a galimoto kuchoka kunja akulephera kupereka misonkho ku bungwe la Mera chifukwa sizikuyenda.

Iwo adati makampaniwo amaitanitsa mafutawo mokwera kwambiri kuchoka kunja ndiye akagulitsa sapezapo phindu zomwe zikuwachititsa kuti azilephera kupereka misonkhoyo.

“Zikapitirira chonchi, mudzanditsimikiza kuti mtsogolo muno osatinso kale wambiri ayi dziko lino lidzabwerera m’nyengo yosowa mafuta ndiye mpomwe katundu amakwera kwambiri mtengo chifukwa amalonda amalowetsa kwambiri kuti apeze mafuta ogwiritsira ntchito,” adatero a Chilenga.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button