Nkhani

Zaka zitatu kwa wogona ndi mbuzi

Bwalo la milandu la First Grade Magistrate la Nkhunga m’boma la Nkhotakota, lagamula a Sandram Lyson, omwe ndi a zaka 27, kuti akakhale ku ndende kwa zaka zitatu atapezeka wolakwa pa mlandu wogonana ndi mbuzi.

Woimira boma pa milandu wochokera pa polisi ya Nkhunga m’bomalo, a Mussa Samuten, adauza bwalolo kuti a Lyson adapamula mlanduwo pa 26 May 2026, m’mudzi mwa Chamalala m’bomalo pamene adagwidwa akugonana ndi chiwetocho.

Izi zidachititsa kuti anthu omwe adampezerera akuchita zolaulazo amugwire ndi kufunsa bwino cholinga chake pogona ndi mbuziyo.

Atakaonekera ku bwalo la milandu la Nkhunga, a Lyson sadachedwetse khotilo koma kuvomereza mlandu omwe adapalamulawo.

Koma mkuluyo adapempha khotilo kuti limuganizire pompatsa chilango chofewa. A Lyson adatsindika kuti sichinali cholinga chawo koma kuti adali ndi chikhumbokhumbo chofuna kugonana.

Tsono kwa iwo ataona kuti pafupi ndi pamene afika, adaona mbuzi yaikazi ili potero, naganiza zogonana ndi mbuziyo pofuna kuthetsa chilakolakocho.

Koma izi sizidakondweretse woimira boma pa milandu amene adati mkuluyo adayenera kulandira chilango chokhwima popeza adanyazitsa bomalo pa zomwe adachitazo, zomwenso zili zosemphana ndi chikhalidwe chathu.

Ndipo popereka chigamulo, First Grade Magistrate Kingsley Buleya adagwirizana ndi ambali ya boma. Motero a Buleya adagamula kuti a Lyson akakhale ku ndende kwa zaka zitatu.

A Lyson amachokera m’mudzi mwa Nkhanje m’dera la mfumu yaikulu Mwanza m’boma la Salima.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button