Mafumu apempha chipinda chochilira amai
Mafumu aku chilumba cha Chisi pa nyanja ya Chilwa m’boma la Zomba adandaula kuti kupanda chipinda chochilira amayi pa chilumbachi chikuyika miyoyo ya amayi pachiopsezo pa uchembere wabwino.
Malinga ndi Gulupu Tchuka, ati zaka zisanu zapitazo khonsolo ya Zomba kudzera ku nthambi ya zaumoyo idawalonjeza kuti awamangira chipindachi.
A Tchukawa ati kutsatira lonjezolo mafumuwa adasankha malo komanso kuwumba njerwa zomangira chipindachi.
“Koma kufika chaka chino palibe chachitika ndipo njerwa zija zayamba kuwonongeka,” atero a mfumuwa.
A mfumuwa ati chipatala chimene ali nacho pafupi kumene kuli maternity yodalilika ndi cha Likangala Health Center chimene chili pa mtunda wa makilomita 15 ndipo amayenera kuwoloka pa nyanja kuti akafikeko.
Malinga ndi mfumuyi, ati kuchoka pa chilumbachi kukafika pa Kachulu Port bwato amalipira K1500 ndipo kuchoka pa Kachulupo kukafika ku chipatala cha Likangala amakwera njinga ya moto ndipo amalipira K3000.
“Kupita ndi kubwera munthu m’modzi imakwana K9000 ndiye kuphatikiza operekeza mayi oyembekezerayu imakwana pafupifupi K18,000 zimene amayi ochepekedwa amangoberekera pakhomo,” atero iwo.
Mayi Elizabeth Kanjo amene ali ndi ana awiri ati mwana wawo oyamba adaberekera pakhomo iwo ndi amunawo atalephera kupeza ndalama zowolokera pa nyanja.
Iwo ati pa chilumbachi pali nyumba imene idasandutsidwa chipatala ndipo mu chipatalacho muli chipinda chimene chidayikidwa kuti amayi aziberekera.
Koma a Kanjo adandaula kuti chifukwa chakuchepa kwa nyumbayo chipindachi chidawandikana ndi polandilira mankhwala a matenda osiyanasiyana ndipo pamadzadza anthu.
“Ndiyetu chilichonse chochitika pobereka chimamveka kunja zimene zimachitsa amayi ngati alibe ndalama kupanga chiganizo chokaberekera pakhomo akawuzidwa kuti akaberekere kutsidya kwa nyanja,” atero iwo.
Poyankhulapo pa nkhaniyi, mkulu wa anamwino komanso azamba m’bomalo a Joseph Zulu avomereza kuti njerwa zinaumbidwadi.
A Zulu ati khonsoloyi ili pakalikiliki kusaka ndalama zomangira chipindachi kuti mavutowa athe.
“Ndi zoonadi pa chilumbachi chipinda chochilira amayichi chikufunika,” anatero