Kafukufuku wa ndege wayamba
Amalawi tsopano maso ali gaaa pa komiti yapadera ya ku Nyumba ya Malamulo yomwe ikufufuzanso chomwe chidachititsa ngozi ya ndege ya asilikali yomwe idapha wachiwiri wakale kwa pulezidenti a Saulosi Chilima ndi Amalawi ena 8 pa 10 June 2024.
Kafukufukuyo ndi wokumba kufuna kuona ngati zotsatira za akafukufuku ena awiri omwe adapeza kuti chifunga ndicho chidachititsa ngoziyo ndi zoona kaamba koti Amalawi ena amang’ung’udzabe kuti pali mafunso ena omwe zotsatirazo sizidayankhe.

Wapampando wa komitiyo a Walter Nyamirandu Manda ati pakutha pa kukumbako, Amalawi ayembekezere mayankho omwe akhala akusowa kwa zaka ziwiri tsopano ndipo ati choona chenicheni chidzadziwika pamapeto pake.
“Tateremu ntchito yayambika ndipo sitisiya mbali iliyonse yokhudzidwa pakafukufuku ameneyu. Uyuyu ndi kafukufuku wachitatu ndipo dziko latikhulupirira kwambiri kuti tipeze mayankho omwe akhala akufuna chichitikireni ngoziyo,” adatero a Nyamirandu.
Ntchitoyo idayamba Lolemba pomwe komitiyo idakayendera bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe kuti ikamvetsetse zina mwa zomwe zimachitika pabwalo la ndege ulendo usadayambe kuti ikadzayamba kuitana mboni idzakhale ikudziwa zomwe zikukambidwa.
A Nyamirandu adati ulendowo udakonzedwa polingalira kuti akadaulo a za ndege kumeneko aunikira komitiyo kuti izidziwa molowa pa kafukufukuyo komanso ndege yomwe ikufufuzidwayo idanyamukira pa bwalolo.
Woyang’anira ntchito za pabwalolo a Gift Matewere adatambasulira komitiyo momwe zimakhalira kuyambira pokonzekera ulendo, momwe uthenga umayendera pakati pa oyondetsa ndege ndi akuluakulu pa bwalo la ndege kufikira kuti ndege yafika komwe imapita.
“Ntchito yathu siyithera poti ndege yanyamuka basi, timailondoloza momwe ikuyendera ndipo timakhala tikulumikizana ndi woyendetsa mpakana ikafike komwe imapita n’kulandira chitsimikizo kuti yafika bwinobwino,” adatero a Matewere.
Lachiwiri, komitiyo idali ku nkhalango ya Chikangawa komwe kudagwera ndegeyo komwe akuluakulu a nkhondo ndi apolisi omwe adatenga gawo pokasaka ndegeyo itagwa adailongosolera momwe zidakhalira pa tsikulo ndipo kenako adakayendera bwalo la ndege la Mzuzu.
Koma Amalawi ena ati kafukufukuyo akadzatulutsa zotsatira ngati zomwe ena adapeza kale ndiye kuti palibe chomwe chachitika kuposa kusakaza ndalama za boma.
“Ilili likhale phunziro chifukwa boma lililonse pakakhala nkhani zofunika kufufuza, ndondomeko zomwe amapanga zimakhala zosapatsa chiyembekezo mpake zinthu zikasintha, obwerawo amayambiranso koma izizi zimangotionongera ndalama,” atero a William Kawokera.
Mkulu womenyera anthu ufulu a Michael Kaiyatsa adati n’kofunikira kwambiri kuti komitiyo ikhale ndi ukadaulo wa za maulendo a ndege kuti ikamachita kafukufuku wake isamaone za chilendo m’mayankho omwe izilandira kwa mboni zina.
“Kafukufuku pa nkhaniyi adachitika kale kawiri konse ndi komiti yomwe apulezidenti omwe adalipo nthawiyo a Lazarus Chakwera adakhazikitsa komanso akadaulo a za ndege a ku German omwe zotsatira zawo sizidasiyane kwenikweni.
“Kafukufuku yemwe akuchitika panoyu ngofuna kutsimikizadi ngati zomwe adapeza enawo n’zoona kapena ayi ndiye ofufuzawo ngofunika kukhala ndi ukadaulo pa za ndege kuti asadzasochezedwe mkatikati,” adatero a Kaiyatsa.
Naye mkulu wa mabungwe omwe ali pansi pa National Advocacy Platform a Benedicto Kondowe omwenso ndi woimiraena pa milandu adati chomwe chikufunika pa nkhani yonseyi ndi chilungamo ndiye mwina muli monse momwe kafukufukuyo angayendere bola zotsatira zake zidzakhale za chilungamo.
“Chomwe chikufunika apapa kuti nkhani imeneyi ithe ndipo anthu akhutire n’kukhazikika pansi ndi chilungamo, kafukufukuyu akuyenera kuonetsa ngati zomwe tidamva poyamba n’zoona kapena ayi osati tidzayambirenso kafukufuku wina mtsogolo,” adatero a Kondowe.
M’mweziwa February, apulezidenti a Peter Mutharika adalamula kuti kafukufuku wa ngoziyo achitikenso ndi Nyumba ya Malamulo nduna ya za chilungamo a Charles Mhango itaunika malipoti awiri oyambirira n’kuwadziwitsa kuti muli mafunso ena osayankhidwa.



