Aphungu ayembekezere mtsutso wokhetsa thukuta
Pomwe mkumano wa aphungu udayamba Lachiwiri pa 7 July, 2026, nkhani mkati mwa sabatayi zasonyeza kuti mbali yomwe siidakonzekere bwino ituluka thukuta zokambiranazo zikamalowa mkatikati.
Izi zaonekera pomwe mtsogoleri wa nyumbayo a Jappie Mhango ati zokambiranazo zikhazikika kwambiri potsiriza mkute womwe udatsalira pa mkumano wapitawo pomwe mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Simplex Chithyola Banda adati pali madengu a nkhani zomwe boma likuyenera kufotokoza bwino.

Mwazina, a Chithyola Banda anati otsutsa akufuna kuti boma likalongosole za tsiku lomwe ndalama za chitukuko (CDF) ziyambe kufika, momwe boma lakukonzekera mphepo ya El Nino, momwe chuma chikuyendera komanso za Amalawi omwe akuthamangitsidwa m’dziko la South Africa.
Izi zikutanthauza kuti kupatula zomwe boma lakonzekera kukapereka m’nyumbayo kuti aphungu akambirane, likonzekelenso kukafotokoza tsatanetsatane wa nkhani zina zikuluzikulu zomwe otsutsa akonza.
Kutengera ndondomeko ya ku Nyumba ya Malamulo, boma limapita ndi zokambirana za masiku anayi sabata ili yonse pomwe otsutsa amakhala ndi mpata opititsa nkhani zawo Lachinayi lili lonse, kutanthauza kuti zomwe a Chithyola Banda akunena zikapeza mpata m’masikuwo basi.
Apanso nkhawa ndiyonena kuti aphungu otsutsa bomawo akakhala ndi masiku atatu okha pa masiku 24 omwe mkumanowo uchitike ndipo akadaulo ati nyumbayo ikuyenera kukagwiritsa ntchito masikuwo pokambirana nkhani zofunika.
Zina mwa nkhani zofunikazo ndizokhudza, CDF, lipoti la hotela ya Amarallis ndi mavuto a zachuma omwe akupangitsa kuti anthu ambiri azilephera kupeza zofuna za pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.
Poyankha mafunso a nyuzipepala ya The Nation ya Lachiwiri, kadaulo ku sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) a Horace Phiri adati aphungu akapane boma pa momwe lakonzekelera kudzathana ndi mphepo ya El Nino.
“Za mphepo ya El Nino ikubwerayi idadziwika nthawi yabwino ndiye boma likuyenera kulongosola bwino momwe lakonzekelera chifukwa mphepoyi idzabwera ndi zotsatira zoopsa monga njala kaamba ka kusakolola mokwanira.
Kadaulo pa zachuma ku sukulu ya Mzuzu University a Christopher Mbukwa adati pa zokambiranazo, aphungu asayiwale nkhani yokonzekera ulimi wa mthilira kupangira mphepo ya El Nino.
“Ndi malipoti a El Nino, aphungu akungoyenera kukambirana za momwe anthu ovutikitsitsa angadzathandizidwire. Pakhoza kukhala njira zambiri zodzathandizira kuti njala isadzavute kwambiri komanso anthu asadzavutike kwambiri,” adatero a Mbukwa.
Amalawi ena omwe adacheza ndi Tamvani mkati mwa sabatayi ati akugwirizana kwambiri ndi zomwe akadaulo anena komanso ena awonjezera kuti nkhani ya kukwera kwa fizi za msukulu za ukachenjede ikakambidwe.
A James Kanyangala aku Area 25 ku Lilongwe adati aphungu asakalephere kukambirana nkhani ya fizi za msukulu za ukachenjede zomwe zakwera kwambiri.
“Nkhani ya fizi yokha akaikambirane chifukwa yakwera udyo. Ndikudziwa kuti ali mpothawira poti amapereka ngongole za fizi, komatu nane ndadutsa momwemo ndipo ndikudziwa kuti si ophunzira onse omwe amapeza nawo mwayi wa ngongole zimene zija,” atero a Kanyangala.
A Jaquerine Kulamkono aku Sector 7 ku Area 25 komweko ati sakufuna kuti azikangomvera nthano ndi nchedzera za aphungu, koma nkhani zenizeni zomwe zikuvulaza ndi kupereka nkhawa kwa Amalawi za komwe akulowera.
“Pali nkhani zambiri zomwe zikukhudza Amalawi, koma atakagwiritsa ntchito bwino nthawi, akhoza kukakambirana zakupsa pakutha kwa mkumano wawowo. Komanso ulendo uno, lipoti la hotea ya Amarallis atipatse,” adatero a Kulamkono.



