Nkhani

A Mpesi atula pansi udindo

Pomwe kwatsala masiku 30 enieni kuchoka lero kuti chisankho chapadera m’madera angapo chidzachitike, mkulu woyendetsa zisankho ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) a Andrew Mpesi atula pansi udindo wawo.

 A Mpesi adatula pansi undindowo Lachiwiri koma wapampando wa bungwe la MEC a Annabel Mtalimanja ati anthu m’madera momwe mukuchitika chisankhochi asade nkhawa chifukwa chisankho chidzachitika a Mpesi asadachoke.

Adazitaya: A Mpesi

“A Mpesi adatula pansi udindo pa 24 May 2026, koma akhala akugwirabe ntchito mpaka pa 21 August 2026. Pamiyesi itatu imeneyi akhala akugwira ntchito yawo monga mwa nthawi zonse uku akupanga chilinganizo ndi yemwe adzamusiire ofesi,” adatero a Mtalimanja.

Izi zikutanthauza kuti iwo adzayendetsa chisankho chomwe chikuyembekezeka kudzachitika pa 30 June 2026.

A Mpesi adalowa ku MEC ngati woyendetsa zisankho mchaka cha 2022 nthawi ya ulamuliro wa Malawi Congress Party (MCP) ndipo chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) sichidavomereze kusankhidwa kwawo powaganizira kuti ndi wotsatira MCP.

Ngakhale adakokedwa ndi lamulo pa nkhani yokhudza galimoto za MEC mu March chaka chino, a Mpesi ayamikiridwa ndi bungwelo kaamba kaukadaulo wawo poyendetsa zisankho komanso pakutsogolera bwino ntchito yogawanso madera a aphungu kuchoka pa 193 kufika pa 229.

Pakalipano, kampeni ya chisankhocho ili mkati ndipo amayi, achinyamata ndi aulumali awamema kuti alimbe mtima n’kutengapo gawo poima m’maudindo.

Izi zikudza pomwe kudadziwika kuti pa chisankho chapadera cha pa 17 March 2026 magulu atatuwa makamaka amayi sadaonetse chidwi moti m’madera ena monga ku Blantyre, padalibe mayi ngakhale mmodzi pa opikisana pampando wa phungu.

Polengeza zotsatira za chisankhocho, a Mtalimanja adatula nkhawa kuti ngati amayi apitirize kudzionera pansi ndiye kuti azisowa okawanenera zofuna zawo.

“Ndi bwino kuti amayi tizilimba mtima n’kumatenga nawo gawo chifukwa timakhala ndi zofuna zathu zomwe mwina abambo sangakatinenere koma tokha, pa chisankho changothachi, amayi sitidaonetse chidwi chofuna mipando,” adatero a Mtalimanja.

Koma mmodzi mwa omenyera ufulu wa amayi kuti azikhala m’mipando Mayi Martha Kathewera Banda adati zina mwa zotsamwitsa amayi ndi nkhanza za m’zipani, zitonzo m’midzi komanso kuperewedwa kwa amayi pa nkhani za chuma.

“Nthawi zinatu zinthuzi zimayambira m’zipani. Umatha kuona kuti m’chipanimo amayi sakupatsidwa maudindo ndiye okha amadzichepsa kuti ngati akumanidwa udindo m’chipani nanga akalandira thandizo lokwanira pa chisankho?” adatero a Banda.

 Iwo adatinso zotsatira za chisankho cha pa 16 September 2025 pomwe mwa mipando ya aphungu 229 amayi 49 okha ndiwo adapeza mipando zidagwetsa amayi ambiri ulesi polingalira kuti mwina anthu akadalibe nawo chikhulupiriro.

 Koma wapampando wa mabungwe oona kuti chisankho chikuyenda bwino a Civil Society Elections Integrity Forum (CSEIF) a Benedicto Kondowe adati ndondomeko yatsopano yolola amayi, achinyamata ndi aulumali kulipira theka la ndalama zofunira kupikisana nawo ikadawamema maguluwo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button