Front PageNkhani

Amangidwa zaka 14 atagonana ndi mwana

Listen to this article

Bwalo la milandu ku Balaka lalamula a Steven Maluwa a zaka 24 za kubadwa kuti akakhale kundende zaka 14 kaamba kopezeka wolakwa pa mlandu oganana ndi mtsikana wa zaka 17.

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’bomalo a Mphatso Munthali, woimira boma pa mlanduwo a Winfred Chikhobili adauza bwalolo kuti wodandaulayo adachitidwa chipongwecho pa 1 February 2024 usiku pomwe amaperekeza mnzake.

Iwo adati wodandaula adakumana ndi mkuluyo yemwe adayamba kumuthamangitsa uku akumugenda zomwe zidachititsa kuti wodandaulayo agwe.

“Izi zidapereka mpata kwa mkuluyo kuti amupeze n’kuyamba kumuvula wodandaulayo mpaka kuchita naye za dama kawiri momukakamiza kenako kumuopseza kuti amupha ngati angadziwitse aliyense za nkhaniyo.

“Atafika kunyumba odandaulayu adafotokozera makolo ake zomwe zidachitikazo ndipo iwo adazafotokoza kupolisi ya Kankao komwe wodandaulayo adapatsidwa kalata yoti akapimidwe ndi chipatala cha Kankao komwe zidatsimikizika kuti msungwanayo adagwiriridwa ndipo apolisi adamanga mkuluyo,” adatero a Munthali.

Poonekela m’bwalolo, Maluwa adakana mlanduwo zomwe zidachititsa woimira milandu kubweretsa mboni 7 zomwe zidapereka umboni wosonyeza kuti mkuluyo adapalamuladi mlanduwu.

Pofuna kuti bwalolo limufewetsere chilango Maluwa adapempha bwalolo kuti lisamupatse chilango chachikulu potengera kuti banja lawo limadalira iyeyo komanso kuti ndi koyamba kupalamula.

Koma woimira boma pa mlandu adapempha bwalolo kuti lipereke chilango chokhwima ponena kuti milandu yonga iyi ikuchulukira m’bomalo.

Popereka chigamulo, woweruza Phillip Chibwana adagwirizana ndi woimira boma pa mlanduwu ponena kuti milandu yotere ikuchuluka kotero adalamula a Maluwa kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka 14 ngati njira yoti ena atengere phunziro. A Maluwa amachokera m’mudzi mwa Chimpakati, mfumu yaikulu Chanthunya boma la Balaka.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button