Asafuna kusaina pangano osamuvotera
Kampeni ya zisankho za mtsogoleri wa dziko lino, aphungu a Nyumba ya Malamulo ndi makhansala yafika pa mwana wakana phala.
Atsogoleri akulonjeza zinthu zambiri moti zina ukamva umangoti kamba anga mwala ndithu n’kumadzifunsa kuti koma iwowa adzazikwaniritsa bwanji zimenezi?
Pa chifukwa ichi, Amalawi ayenera kuunika ndi kusanthula mozama malonjezo omwe atsogoleri akupanga, n’kumawafunsa mafunso n’cholinga choti afotokoze njira zomwe azigwiritse ntchito pokwaniritsa malonjezowo.
Tiyamikire mabungwe a Malawi Electoral Commission (MEC), Oxfam ndi Women Legal Resource Centre (Wolrec) posaina mapangano ndi zipani za ndale, komanso anthu omwe akuima pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino.
Mabungwewo achenjera kaamba koti alemba zinthu zomwe ayembekezera kuti atsogoleriwa adzatsatire kapena kukwaniritsa n’kuwauza kuti asayinire pangano.
Achita izi poopa kuti mawa atsogoleriwa atha kumadzanjanja kuti sadalonjeze zomwe mabungwewa akufunazo. Pa nthawi ino ndi akapolo a anthu koma akasankhidwa amasanduka mabwana – zomwe sizikuyenera kutero.
Mapanganowa ndi amene adzawathandize pochita kalondolondo wa malonjezo omwe atsogoleri akupanga panopa.
M’mbuyomu anthu ambiri akhumudwa kaamba koti atsogoleri a ndale sakwaniritsa malonjezano awo moti ena adalumbira kuti sadzavotanso.
Yankho sikukana kuvota koma kupeza njira zabwino zolondolera malonjezo omwe atsogoleri akupanga pa nyengo ya kampeni yomwe tili nayo panoyi.
Anthu mogwirizana ndi mafumu awo alembe zitukuko zomwe amafuna m’madera mwawo.
Akatero ayitane atsogoleri omwe akupikitsana m’modzi-m’modzi ndi kusayinirana nawo mapangano.
Izi zidzawathandiza kuchita kalondolondo kampeni ikatha ndipo ntchito yokwaniritsa zitukukozo ikayamba.
Chaka chino ovota sagona mtulo!
Demokalase ndi ulamuliro wa anthu. Anthu ayenera kufotokoza zofuna zawo osati mtsogoleri kumawauza zomwe akufuna.
Anthu ali ndi nzeru zokwanira kufotokoza zofuna zawo.
Ichi n’chifukwa chake anthu alembe zofuna zawo n’kusainitsa atsogoleri awo.
Oxfam ndi Wolrec idachita mbali yawo, koma n’kovuta kuti mabungwewa asaine pangano ndi khansala, komanso phungu aliyense.
Ntchito imeneyi asiira anthu, mafumu ndi magulu omwe akugwira ntchito ku maderawo kuti ndiwo achite zimenezo.
Tisalole kusiyana kwa zipani kuti kutigawe.
Tiyeni tigwirane manja ndi kupempha makhansala ndi aphungu omwe akuima m’madera mwathu kuti asaine pangano kuti tisadzavutike pochita kalondolondo wa malonjezano awo.
Ngati safuna kukwaniritsa zofuna zathu, tisadzawavotere chifukwa amenewo sakufuna kutumikira anthu, koma kudzitumikira okha.
Kampeni yabwino yagona pa zofuna za anthu.
Pa kampeni atsogoleri azingouza anthu njira zomwe adzagwiritse ntchito pothana ndi mavuto a anthu.
Posachedwapa tidacheza ndi atsogoleri, mafumu ndi mkhalakale pa ndale m’maboma a Machinga, Zomba ndi Mulanje omwe adatifotokozera mwa tsatanetsatane kuti Amalawi sakwanitsa kuchita kalondolondo wa malonjezo omwe atsogoleri a ndale amachita nyengo ya kampeni.
Adatiuza kuti makomiti a chitukuko a m’madera ndiwo nthawi zina amakwanitsa kulondola zomwe makhansala ndi aphungu adalonjeza.
Izi n’zabwino, koma kalondolondo wa malonjezo omwe atsogoleri amapanga pa nthawi ya kampeni akuyenera kuchitikanso ndi eni ake – anthu m’midzi ndi m’madera kuti atsogoleri athu azikwaniritsa zomwe akulonjeza nthawi ya kampeni.
Padakalipano, atsogoleri akamalonjeza, anthu azilemba ndi kuwapempha asayinire.
Akakana ndiye kuti amenewo si atsogoleri, koma atambwali ofuna kukolola pomwe sadalime – ndipo tichenjere nawo.
Osawavotera chifukwa adzatiliza!
Tikungofunika chimvano cha mavu kuti izi zitheke!