Asambwaza othawa kulima

Listen to this article

Mkulu wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi la the Department of Disaster Management Affairs (DoDMA) a Charles Kalemba ati Amalawi kukhala ndi njala n’kufuna popeza ali nazo zonse zoyenera kuwachotsa mu nsinga za njala.

Iwo adalankhula izi pa Muona Resources Centre m’boma la Nsanje Lachisanu pakutha pa ulendo wawo woyendera masikimu a Ntolongo m’dera la T/A Tengani, ndi Makhaphwa kwa T/A Mlolo m’boma la Nsanje.

Iwo adati nthambiyo idapeza thandizo kuchokera ku Africa Development Bank (AfDB) kudzera ku chilinganizo cha Post Cyclone Idai Emergency Recovery Project (PCEIRP) zomwe adakonzera masikimu awiriwo komanso ya Mkulowamitete kwa Ndamera ndi Nyamphembere kwa Mbenje zimene zidaonongeka ndi namondwe wa Idai.

“Ndamva chisoni kwa a Tengani komwe alimi sakuonetsa chidwi cholima m’sikimu ya Ntolongo yomwe tidawapatsa pomwe anzawo achoka nsinga za njala ndi kusiya kukhala m’magulu a zolandira,” adatero iwo.

A Kalemba adati n’zomvetsanso chisoni kuti ena akuba zipangizo zina pa sikimu monga makina a mphamvbu ya dzuwa.

Iwo adati: “Timayenera kuphunzira kwa anzanthu m’maiko omwe ndi zipululu komwe alibe nthaka yoti alime monga Israel, Syria, Lybia, United Arab Emirates ndi ku Egypt koma amakolola kwambiri pogwiritsa ntchito nthaka yokatenga kwina.

“Ndinene moona mtima kuti kukhala ndi njala kuno kwathu ku Malawi ndi kufuna komanso kusaganiza bwino. Tili ndi nthaka yabwino komanso madzi womwe timangowaona pofuna kusakhala m’matope koma kumapitilira kukhala wosaka. Timayenera tidzimvereko chisoni ndi kusintha pa kaganizidwe monga masomphenya achitukuko a dziko lino a Malawi 2063 akunenera.”

A Kalemba apempha khonsolo ya boma la Nsanje kuti ichotse wonse omwe sakufuna kulima m’masikimu a Ntolongo ndi Makhaphwa mu ndandanda wa olandira zinthu zochokera kuboma kuphakizapo mtukula pakhomo ponena kuti nthambi yawo siyikufuna kuthandiza anthu aulesi.

Gogo Tengani ati aika sabata imodzi kuti anthu ake ayambe kulima m’sikiyimuyo yomwe akhulupilira kuti idzathetsa vuto la njala lomwe amakumana nalo.

“Tichotsa aliyense kuyambira kukomiti yoyendetsa sikimuyi kufikira kwa alimi ngati sakuonetsa chidwi chofuna kulima ndipo tipeza anthu ena kuti adzayambe kulima musikimuyi,” adatero iwo.

Wapampando wa sikimu ya Ntolongo a Christopher Thomu anati alimi 555 omwe 307 ndi abambo, akukumana ndi vuto la madzi a mchere pazitsime zitatu mwazitsime 7 zomwe zimathirira pa mahekitala 88.

“Talima kawiri konse koma chimanga chathu chimafa chikafika m’maondo kaamba ka madzi a mchere. Tikawauza alangizi palibe chomwe akutithandiza koma tili ndi khumbo lofuna kulima,” adatero iwo.

Naye wapampando wa sikimu ya Makhaphwa pomwe pali mijigo 12 koma ikugwira ntchito ndi 6 a David Mainje adati alipo alimi 720 (abambo 350) akulima chimanga koma vuto ndi umbava wa mapanelo a sola.

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button