Lamulo la za umoyo likulephera kuluma
Lamulo la za umoyo la m’chaka cha 2019 likulephera kugwira ntchito kaamba koti lilibe mndondomeko.
Cholinga cha lamuloli chidali kukhwimitsa ntchito zaumoyo poteteza mankhwala, kuchepetsa mchitidwe wogulitsa mankhwala osayenera ku boma, komanso kuletsa mankhwala osavomerezeka azitsamba.

Mkulu wa bungwe la Malawi Health Equity Network (Mhen) a George Jobe wauza Tamvani kuti n’kovuta kugwiritsa ntchito lamuloli opanda ndondomeko.
Amalawi amayembekezera kuti lamuloli likayamba kugwira ntchito yake mchitidwe woba mankhwala, wogulitsa mankhwala osayenera, komanso woti nthawi yawo yogwira ntchito yatsala pang’ono kutha (expired drugs) uchepa.
A Jobe adati zaka 7 zapita koma unduna wa za umoyo ukukumanabe ndi mavuto omwe umakumana nawo mu 2019 chifukwa chopanda ndondomeko.
“Ndikudabwa kuti zikutenga nthawi kukhazikitsa ndondomeko, kunena zoona takhalira lamulo lofunikira kwambiri.
“Timayembekezera kuti lamuloli likhala polisi yaikulu pa ntchito yoteteza mankhwala ndikuletsa mchitidwe uliwonse waukambelembele m’zipatala zathu,” adatero a Jobe.
Iwo adati mankhwala ambiri a boma amabedwa, kuzembetsedwa, kugulitsidwa, komanso nthawi zina “timagula mankhwala osayenera ndipo amangotaidwa”.
A Jobe adati kaamba koti lamuloli silikugwira ntchito, okuba mankhwala amalandira zilango zofewa akagwidwa.
“Lamuloli likadzayamba kugwira ntchito, aliyense wokhudzidwa ndi kubedwa kwa mankhwala azidzalandira chilango chokhwima,” iwo adatero.
Wapampando wa komiti ya za umoyo ya m’Nyumba ya Malamulo a Anthony Masamba adati komiti yawo ikudziwa zoti lamulolo likulephera kuluma kaamba koti lilibe ndondomeko.
“Zimenezo tikuzidziwa. Mavuto onsewa adza kaamba kochedwa ndondomekozo. N’chifukwa chake komiti yathu idaunika ndi kusindikiza zina mwa ndondomekozo,” adatero a Masamba.
M’chaka cha 2022 ndondomeko zokhudza ndalama zoyenera kulipira ndi kalata za chilolezo zidapangidwa n’kusindikizidwa.
Koma a Jobe ndi akadaulo ena a za umoyo akuti ngakhale ndondomezo zidasindikizidwa, n’zosakwanira kupepeka mphamvu ku lamulolo.
Unduna wa za umoyo sudatiyankhebe chomwe chikuchedwetsa ndondomekozo.



