Editors Pick

Mayeso alembedwanso?

Listen to this article
Ophunzira kulowa m'kalasi kukalemba mayeso
Ophunzira kulowa m’kalasi kukalemba mayeso

Unduna wa Maphunziro wati ukudikira chikalata chochokera kubungwe loona za mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) usadalengeze ngati mayeso a Malawi School Certificate of Education (MSCE) angapitirire kapena ayi.

Mneneri wa undunawu Rebecca Phwitiko adanena izi kutsatira zomwe ena amapempha undunawo kuti uimitse mayesowo chifukwa adabooka ndipo ophunzira ena adagwidwa ndi malikasa mayeso  asadalowe m’chipinda cha mayeso.

Phwitiko Lachitatu adati Maneb ikuyembekezeka kutulutsa chikalatacho Lachinayi usadagamule za tsogolo la mayesowa.

“Vuto lakubedwa kwa mayeso limadza chaka ndi chaka. Boma likuyesetsa kuchepetsa vutoli ndipo mtsogolomu izi zidzakhala mbiri yakale. Koma padakalipano tidikire Lachinayi kapena Lachisanu, timve kafukufuku wa Maneb wayenda bwanji.

“Tidzanena ngati pangafunike kuti mayesowa adzalembedwenso koma ophunzira apitiriza kulemba,” adatero Phwitiko.

Mkulu wa bungwe la Maneb Roy Hauya wati bungweli likufufuza komwe mayesowa adatulukira chifukwa bungwe lawo lidaika chitetezo chokwanira kuti pasakhale zoonera mayeso.

“Sindikumvetsa kuti mayesowa atulukira pati chifukwa chitetezo ndiye chidalipo. Mayeso onse adapangidwa ku Mangalande ndipo adachoka kumeneko nkumapita m’malo olemberamo mayeso ndipo palibe pepala lililonse lomwe Maneb idagwirapo ntchito,” adatero Hauya.

Iye adatsutsa mphekesera yomwe ikumveka kuti bungweli lidasindikiza mayeso osakwanira ku Mangalande ndipo amachita kukopera ena pa makina konkuno, zimene zidachititsa ena kuti awapeza msanga.

Iye wati bungweli litulutsa zotsatira za kafukufuku yemwe limachita mogwirizana ndi apolisi.

Malinga ndi mkulu wa mgwirizano wa mabungwe opititsa patsogolo ntchito za maphunziro m’dziko muno la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati Maneb iyenera kubwera poyera ndi kuuza Amalawi pamene vuto lakubedwa kwa mayeso a MSCE lafika.

Iye adaloza chala Maneb, ati bungwelo likubisira Amalawi chilungamo pa zavutoli lomwe wati lafika podetsa nkhawa.

“Pali mavuto ambiri omwe angabwere chifukwa cha nkhani ya mtunduwu monga kukozanso mayeso ena zomwe zingaononge ndalama zambiri komanso kusiya choncho ndiye kuti maphunziro alowa pansi kwambiri,” adatero Kondowe.

Iye adati ophunzira amapeza mayeso atangotsala pang’ono kuwalemba ndipo akumakhala atapeza kale mayankho ake. Izi wati zikudza chifukwa cha kuchepa kwa ndalama zomwe apolisi ndi aphunzitsi oyang’anira mayesowa amalandira, zomwe zimachititsa kuti agulitse mayesowo.

“Tangoganizani kuti munthu akuyang’anira mayeso koma ndalama zomwe akupatsidwa ndi zochepa, mwinanso kutenga chinthawi chachitali kuti apatsidwe ndalamazo choncho pangalephere kuchitika za chinyengo?” adatero Kondowe.

Mkulu woyang’anira za chitetezo ku Maneb, Robert Harawa, komanso apolisi adatsimikiza kuti ophunzira ena omwe akulemba nawo mayeso a MSCE adapezeka ndi mayesowa asadalembedwe.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi m’dziko muno, Kelvin Maigwa, adatsimikiza kuti ophunzira ena adamangidwa m’zigawo zonse za dziko lino chifukwa cha nkhaniyi ndipo adati apolisi mogwirizana ndi a bungwe la Maneb ali pa kalikiliki kufufuza ngati ophunzira apeza mayeso omwe sanalembedwe.

“Ubwino wake ophunzira ena omwe adamangidwa avomera kuti adali ndi mayeso omwe amayembekezera kulemba koma chomwe chatsala ndikuti tipeze komwe mayesowo adachokera,” adatero Maigwa.

Kondowe wati chaka chino chokha mapepala a mayeso 7 apezeka kale ndi ophunzira omwe akulemba mayeso ndipo wati izi zikusonyeza kuti vutoli ndi lalikulu kwambiri, lofunika boma litalowererapo.

Josephine Ngwira, yemwe mwana wake ndi mmodzi mwa ophunzira vomwe akulemba mayesowa, wati bungwe la Maneb likuyenera kudzikonza bwinobwino kuti tsogolo la maphunziro lisapite pansi.

Iye wati ndi zokhumudwitsa kuti anthu a nzeru oyenera kulandira ulemu wawo amaoneka ngati opanda nzeru chifukwa cha anthu omwe amabera mayeso ndi kumakhoza bwino.

“Panopa makampani amadandaula kuti achinyamata ochokera kusukulu zaukachenjede sadziwa kugwira ntchito. Sikuti zimakakhota kusukulu za ukachenjede kuti kulibe maphunziro abwino koma kumapita anthu osayenera omwe amabera mayeso ngati mmene zakhaliramu.

“Chodabwitsa kwambiri ndichakuti kolemba mayesoko kumakhala oyang’anira komanso a chitetezo kodi onsewa ntchito yawo ndi chiyani? Akatero mumva akuti mayeso alembedwenso kungowononga ndalama ndi nthawi basi,” adatero Ngwira.

Related Articles

Back to top button