Mikanda ndi yovala paliponse?
Anatche,
Ndithandizeni ine. Kodi ndi zoyenera kuvala mikanda ya m’chiuno kulikonse kumene ukuyenda?
Izi ndafunsa chifukwa ndili m’basi ndinaona mtsikana wina atavala mikanda. Mikandayo inaonekera chifukwa choti anavala kabulauzi kakang’ono ndi buluku.
Mtsikanayu amaoneka kuti akupita ku sukulu. Anatche, ndinali wozizwa kuti mpaka mikanda m’chiuno wa ku sukulu? Koma sukuluyo iyenda pamenepa?
Blantyre.
Wawa,
Sindikudziwa kuti atsikana a masiku ano ndi otani. Mikanda si yofunika kuvala paliponse. Ivalidwe pamalo poyenelala.
Masiku ano tikakwera minibasi timakhala anthu anayi pa mpando. Ndiye zimaoneka kuti timakhala mothithikana kwambiri. Ngati wavala mikanda zimatheka kuti anthu akuyigunda chifukwa chopanikizana.
Mikanda imavalidwa kuti usangalatse mwamuna wako osati aliyense aziyiona kapena kuigunda ayi. Umenewo ndi u vubwa. Komanso ngati wavala mikanda uyenera kuvala mwa ulemu kuti isaonekere.
Mwana wa sukulu sayenera kuvala mikanda. Akupita kokakumana ndi amuna kapena kophunzira?
Dzisungireni ulemu nokha atsikana. Ikaduka zimakhala zochititsa manyazi zedi. Mayi wina wake inamudukila m’banki. Zinali za manyazi kwambiri.
Ndi hule yekha amene angavale mikanda paliponse.
Ndizichita bwanji ine azakhali?
Ndine mayi wa pabanja. Banja lathu latha zaka zinayi. Tonse timagwira ntchito.
Amuna anga amalandira ndalama zambiri ndithu kuposa ine. Iwowa amanga nyumba ya mayi awo komanso anawagulira zifuyo makolo awowa.
Makolo anga ndi ovutika zedi. Makolo anga alibe mtengo ogwila uliwonse. Amai amagulisa masamba kuti mwina zithu zizitheka pakhomo. M’banja mwathu tilipo atatu. Ndine woyamba.
Amuna anga safuna kuti ndalama zanga ndizithandiza nazo kwathu. Ndikafunsa kuti bwanji mukuchita zimenezi amati ine ndili m’manja mwawo.
Amandiuza zoti ndigule pa ndalama yanga. Komatu ine sindichita kaduka akamathandiza kwawo. Nditani pamenepa Anatchereza.
SF,
Mangochi
Zikomo SF,
Banja ndi umodzi komanso banja limalimbitsa ubale. Auzeni amuna mwa ulemu ndi mwa chikondi kuti zomwe akuchitazo ndi zosakomera banja. Kumeneko ndi kudzikonda kwambiri. A
liyense amayenera kuthandiza kholo lake. Ndipo kuthandiza kwambiri n’koti muyenera kuchitira zones limodzi n’kumauzana kuti makolowa tiziwathandiza ndi ndalama mwakuti mbali zonse.
Alipo ena amati iwe kwanu nkolemera ndiye makolo ako ngosayenera kupatsidwa chithandizo. Kumeneko ndi kulakwa kwambiri. Athandizeni ndithu kuti nawo adyeko zamwana wawo.
Ngati amuna anu sakusintha auzeni ankhoswe kuti alowererepo.
Mikanda imavalidwa kuti usangalatse mwamuna wako osati aliyense aziyiona kapena kuigunda ayi. Umenewo ndi u vubwa. Komanso ngati wavala mikanda uyenera kuvala mwa ulemu kuti isaonekere.