‘Nthawi ya mameya ikuchepa’

Listen to this article

 

Katswiri wa zandale, utsogoleri ndi zopereka mphamvu ku anthu, Dr Augustine Magolowondo wati mpofunika kuti boma liunike nthawi yomwe munthu amakhala pampando wa umeya pofuna kupereka mpata woti munthu

akhazikike ndikupanga zooneka.

Mmbuyomu, pamene aphungu amakhala zaka zisanu, makhansala amakhala zaka zinayi ndipo mameyanso amakhala zaka zinayi. Koma malamulo adasintha pomwe makhansala amakhala zaka zisanu ngati aphungu koma amasankha mameya kawiri, kusonyeza kuti amakhala zaka ziwiri ndi theka. Koma akafuna, amatha kupikisana nawonso.

Magolowondo: Azikhala zaka 5

Magolowondo adati kuchokera pomwe munthu wapambana pampandowu, pamakhala nthawi yodzilinganiza ndi ntchitoyi, kenako ayambe kuyigwira ndipo posakhalitsa amangozindikira nthawiyo yatha.

“Zaka ziwiri ndi theka nzochepa kwambiri kuti munthu angapange zooneka chifukwa imagawidwa m’zigawo zingapo komanso pali zitukuko zina zotenga nthawi kuti zitheke ndiye mpovuta kumuyeza munthu panthawi yochepa bola zikadakhala zaka zisanu ngati makhansala kapena aphungu ndi pulezidenti,” adatero Magolowondo.

Iye adati chisankhireni mameya omwe nthawi yawo yangothawa, zinthu m’mizinda zidayendako bwino kuposa momwe zidalili kulibe adindowa ndipo adapereka zitsanzo za misewu yomwe yakonzedwa m’mizinda ikuluikulu ndi kayendetsedwe ka mabizinesi.

Dziko la Malawi lidakhala ndi mameya komaliza pautsogoleri wapakati pa 2004 ndi 2009 ndipo kuchoka apo, kudalibe mipandoyi chifukwa kudalibe makhansala ndipo akatswiri akhala akunena kuti izi zinkachititsa kuti chitukuko chizichedwa.

Pounikira momwe mameya omwe angosankhidwa kumenewa angagwirire ntchito bwino, Magolowondo adati akuyenera kupatula ndale ndi ntchito yawo chifukwa kawirikawiri ndale zimasokoneza ntchito.

“Tikudziwa kuti mameya ndi anthu omwe ali ndi zipani zawo ndipo ali m’mipandoyi kaamba kazipanizo koma mmene zateremu, akuyenera kuiwala za zipani zawo nkuyika mtima pantchito yawo yomwe ndi chitukuko,”

adatero Magolowondo.

Iye adati mayeso aakulu omwe mameyawa akuyenera kusamala nawo ndi kayendetsedwe ka chuma cha m’makhonsolo awo chifukwa aliyense maso amakhala pamenepo ndipo anthu ambiri adaononga mbiri chifukwa cholephera mbali imeneyi.

Iye adatinso chinsinsi china choti asangalatse anthu a m’mizinda yawo, n’kuunika zomwe anzawo adakhonza kuti aonjezerepo komanso zomwe adalephera ndikuwona kuti iwo angakonze bwanji. n

Related Articles

Back to top button