ChichewaFront Page

TIDAKUMANA: ‘Mudali mu Barbershop’

Lidali tsiku Lachisanu masana m’chaka cha 2012 ku Area 25 C ku Lilongwe ndipo kunja kudali kwa dzuwa pomwe Shingrai Nkhoma komanso yemwe tsopano ndi mwamuna wake Wonderful Sakala adakumana pa malo wometera tsitsi, barbershop.

Shingrai atangolowa m’malo wometerawa, adaphana maso ndi Wonderful yemwe pa nthawiyo ankadya tchipisi ndi mnzake, atakhala pa mpando mkati mwa malowa.

Mwatsoka, Shingrai sadapeze mwini wake malowo ndipo pomwe adafunsa mphongo ziwiri zomwe zimadya tchipisizo zidayankha kuti: “Ife sitikudziwa komwe wapita.”

Shingrai adati: “Ndipo pomwe ndimadikira mwini wake yemwe amameta pa malowo, anthu awiriwa anandipatsa mpando kuti ndikhale ndipo ndidakhaladi.”

Chimwemwe ndiye chawo: Shingrai ndi Wonderful. I Chochokera kwa Sakala

Iwo adafotokoza kuti koma patapita mphindi zochulukirapo, mwini wake malowo adafika, ndidametetsa, kulipira, kenako n’kumapita ku nyumba. Ndipo sadalakhunalepo zokhudza ubwenzi.

“Pomwe ndimayenda kupita ku nyumba, sidadziwe kuti wina mwa anthu awiri amadya tchipisi mu babashopu aja akundilondola mmbuyo ndipo ndidamva mawu akuti: ‘Asisi taimani.’ Ndipo ndidaiimadi,” adetro iye.

Ndipo atapatsana moni wa chinyamata mnyamatayo adapempha nambala ya foni.

“Ndidapereka nambalayo ndipo adandiimbira tsiku lotsatira pomwe adafotokoza cholinga chake,” adatero Shingrai.

Ndipo adati akuluwo ankaimba foni tsiku ndi tsiku kwa mwezi ndipo iye, ankayankha monyinyirika.

“Patatha mwezi ndi pomwe mtima wanga udayamba kukhazikika, tsopano ndimayankha foniyo bwino komanso kucheza kwa wina ndi mnzake kudayamba,” adatero iye.

Wonderful naye adati kenako adafunsira ubwenzi ndipo adayamba kudziwana bwino mkati mwawo.

“Pomwe chibwenzi chathu chidayamba, timacheza tsiku ndi tsiku, ndipo zimenezi idakolezera ubwenziwu,” adatero Wonderful.

Iye wati adali ndi khama kuti atenge mkaziyu chifukwa adamukonda kwambiri.

“Ngakhale poyamba amayankha foni yanga monyinyirika, koma ine ndinkadziwa kuti zitha. Ndipo zidatheka, pano tidakwatirana m’chaka cha 2013, mkazi wanga uyu ali apayu,” adatero iye.

Padakali pano banjali likukhala m’boma la Karonga komwe akugwira ntchito zawo zosiyanasiyana

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button