Uncategorized

Zisankho zapadera zanunkhira

Zokonzekera za zisankho zapadera zimene zichitike m’madera ena Lachiwiri likudzali zafika pachimake.

Chisankho chapadera cha phungu wa Nyumba ya Malamulo chichitika m’dera lapakati m’boma la Karonga potsatira imfa ya yemwe adali phungu wa deralo Cornelius Mwalwanda wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP). Ndipo kumadzulo cha kumpoto kwa boma la Lilongwe kuli chisankho chifukwa yemwe adapambana pachisankho cha 2019, Lazarus Chakwera tsopano ndi mtsogoleri wa dziko lino. Chisankho china chili kuwodi ya Makhwira m’boma la Chikwawa.

Woimira UTM Party: Mwenifumbo

Malinga ndi chikalata cha bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), zikalata zoponyera voti zimayembekezeka kufika m’dziko muno dzulo kubwalo la Kamuzu International Airport (KIA).

“Zikalatazo zikangofika zidzatumizidwa kumaderawo kupyolera kumakhonsolo. Tikuyembekeza kuti zipani ndi opikisana onse kuti atumiza nthumwi kuti zikalandire zikalatazo ndi kukaona malo omwe zikakhale motetezedwa,” chidatero chikalatacho.

Ngakhale mavoti akuponyedwa m’madera onsewa, zinthu sizili bwino m’boma la Karonga komwe opikisana awiri a zipani za MCP Leonard Mwalwanda ndi UTM Party Frank Mwenefumbo, akukhalira kutibulana.

Chodabwitsa n’choti awiri mwa opikisana ochokera ku zipani ziwirizo omwe zili mumgwirizano wa Tonse ndi omwe akuchita ziwawa.

Pofika Lolemba m’sabatayi, anthu 14 adali atavulazidwa pa misonkhano yokopa anthu ndipo milandu isanu ndi itatu idatsekulidwa.

Mwa anthuwa, 6 ndi achipani cha MCP, 6 a UTM Party pomwe awiri ndi otsatira oima payekha.

Masiku apitawa otsatira chipani cha UTM Party adamenya ndi kuvulaza anthu awiri otsatira Shackie Florence Nthakomwa yemwe ndi woima payekha.

Anthuwa omwe ndi Fishani Chisiza wa zaka 36 komanso Jonathan Zigana wa zaka 29 adamenyedwa pamalo a malonda a Mwenilondo Lamulungu.

Polankhulapo, Nthakomwa adati zipolowe zachuluka m’madera a Mwenilondo komwe anthu otsatira Mwenifumbo sakufuna kuona mbendera za zipani zina.

“Anyamata anga akumagona panja kulondera mbendera zathu. Koma ine sindikuopa ndipo ndipambana pa zisankhozi,” adalongosola Nthakomwa.

Katswiri pa nkhani za ndale yemwenso ndi mphunzitsi pa sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College adati zipani zomwe zili mu mgwirizano wa Tonse zikufunika kuwauza owatsatira tanthauzo lenileni la mngwirizano ngati zikumenyana chomwechi.

Mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa adati bungwe lake lalandira madandaulo a zipolowe ndipo likuwaunika.

Iye adati izi zikapitilira bungwe la MEC likhonza kuletsa woyambitsa zipolowe kudzaimira nawo pa zisankhozi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button