Chichewa

Anatcheleza: Akundiopseza a gogo wanga

Listen to this article

Akundiopseza Gogo wanga,
Ndili ndi zaka 24 ndipo ndimachokera kwa Kachere mumzinda wa Blantyre koma pano ndili ku Mangochi kumene ndikugwira ntchito m’bala ina.
Ndidakwatirana ndi mwamunayo amene ndidamupeza pabala pomwepo patangotha miyezi. Pano tatha chaka ndi miyezi 4 tili pabanja koma tsiku lina mpaka 2 koloko adali akadali kumowa. Nditaimba foni adandilalatira ndipo adandiuza kuti pali akazi ambiri amenenso amamufuna. Ndidanyamula tanga, koma amandiopseza kuti azindimenya tikakumana.
KM,
Mangochi

KM,
Kuopseza ena ndi mlandu. Mosayang’ana kuti kumbuyoku mumakhala bwanji
muyenera kukanena kupolisi. Uwu ndi mlandu ndithu umene ungachititse
amuna anu akalewo kuona mavuto. Koma nanu a KM, mwamuna wokwatirana naye mungamupeze kubala? Simudamvepo kuti nkhuku yoweta sagula pamsika? Zofunatu izo!

Tatalikana
Gogo,
Ndine mtsikana amene ndili ndi chibwenzi chomwe chimakhala ku Blantyre
pomwe ine ndimakhala ku Mzuzu. Takhala chaka chimodzi osaonana koma
timalankhulana pafoni tsiku ndi tsiku. Ndikamufunsa kuti ubwera liti
kudzandiona amangoti nthawi idzakwana yokha. Kodi ameneyu ali nanedi
chidwi?
FT,
Mzuzu

FT,
Chikondi sichiona mtunda. Zili bwino kuti mumalankhulana tsiku ndi tsiku. Choncho mukulankhulanako mukhoza kuona ngati chikondi chilipo kapena ayi. Komanso dziwani kuti pamene mukutalikana, nthawi zina chikondi chimazilala. Nkuthekatu apa kuti chikondi cha mwamunayo pa inu chikuzilala. Komanso mbali inayo, bwanji inuyo osayesa kunyamuka kuchoka ku Mzuzu nkudzamuona mwamunayo ku Blantyre? Simunanenepo kuti
adakuletsani kuti mukamuyendere ku Blantyre.

Anandilodza
Odi agogo, ndinalodzedwa kwawo kwa mwamuna wanga, ndipo ndinapulumuka mwachisomo. Kwathu anati ndibwerere kubanja koma makolo akuchimunawo akuonetsabe kuti sakundifuna. Ndili ndi mantha chifukwa mwamuna wanga alibe nazo vuto. Nditani?
BN,
Balaka

BN,
Poyamba simudafotokoze kuti mudadziwa bwanji kuti mudalodzedwa. Ichitu
nchifukwa chake boma limanena kuti wotchula mnzake kuti ndi mfiti ayenera
kumangidwa. Nkhani zotere zimangodzetsa udani chabe. Ngati mwamunayo
akuonetsa kuti akukondani, ndi bwino mubwerere, pajatu banja ndi anthu awiri.

Anatchereza,
Ndili pabanja ndi mkazi yemwe akuti ndidamupatsa mimba zaka zisanu zapitazo. Iye adabereka patatha miyezi 8 kuchokera pomwe adandiuza kuti ndamupatsa mimba. Mwanayo sakufanananso ndi ine. Nditani?
LC,
Mzuzu

LC,
Palibenso chimene mungachitetu apa kuthetsa banja chifukwa mukukaikira kuti mwana wa zaka 5 si wanu. Nthawi yonseyi munali kuti? Mwadziwa liti kuti mwanayo sakufanana nanu? Pezani chifukwa china chothetsera banja ngatidi m’banjamo muli vuto, osati zimene mukunenazo.

Ofuna mabanja

Ndili ndi zaka 20 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka zochepera paine. 0996414592

Ndili ndi zaka 26 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 20 ndi 24. 0885471466

Ndili ndi zaka 20, ndikufuna mkazi wa zaka 18 mpaka 20. 0888963917

Ndili ndi zaka 30 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 35 ndi 40. 0994020379

Zaka ndili nazo ndi 33 ndipo ndikufuna mwamuna. 0998501901.

Related Articles

Back to top button
Translate »