Chichewa

Thirani manyowa mwachangu kuti mukolole

Listen to this article

Mmodzi mwa akadaulo a za kafukufuku wa za nthaka ku nthambi ya zakafukufuku wa za ulimi a Peter Mpate akuti kuthira manyowa mwachangu m’munda n’kopindulitsa.

Iwo adati kuthira manyowa mwachangu kumathandiza kuti alowerere bwino m’thaka choncho mlimi akabzala mbewu pomera imapezana ndi chakudya chokwanira ndipo imakula mwamphamvu ndi kubereka bwino.

A Mpate adaonjeza kuti m’zaka zina mvula yoyambirira imatsogozana ndi ng’amba kotero mlimi akathira manyowa moyambirira dothi limakwanitsa kusunga chinyontho kwa nthawi yaitali.

“Zotsatira zake mbewuzo zimapirira ku ng’amba ndipo sizipserera,” adafotokoza motero.

Malingana ndi katswiri wa zaulimi wa mbewu a Hermes Mphambano, mbewu za m’munda mmene mwathiridwa manyowa zimakhala kwa sabata ziwiri osaonongeka kukachita ng’amba.

Yambanipo kuthira manyowa m’munda mvula isadagwe

“Manyowa amasunga chinyontho komanso mbewu zimene zalimidwa pa dothi la manyowa zimakhala za mphamvu ndipo zimakula mwachangu,” adafotokoza motero.

Kuonjezera pa izi, mlangizi wa mbewu wa m’chigawo cha za ulimi ku Thiwi m’boma la Nkhotakota a Frank Bango adaonjeza kuti kuthira manyowa nthawi yabwino kumathandiza kupewa kuchulukitsa ntchito pamene mvula yagwa.

Iwo adati kuthira manyowa ndi ntchito yaikulu chifukwa amafunika ochuluka kuti akwanire munda onse choncho mlimi akachedwa zotsatira zake amangothira chigawo chochepa kwinako n’kusiya.

“Mvula ikagwa zochitika ku munda zimachuluka zotsatira zake kuthira manyowa kumasiyidwa kaye mmbuyo choncho popewa izi ndi bwino kuthiriratu.

“Kwa alimi amene amathirabe manyowa osapsa, kuthira mochedwa kumaika pachiopsezo mbewu zawo chifukwa amakaotcha mbewu zija,” adatero mlangiziyo.

Chifukwa choti mayi Eneles Timothy a ku Ntonda m’boma la Blantyre amadalira manyowa pa ulimi wake, amayesetsa kukonza ndi kuthira manyowa m’munda mwake mwachangu.

Iwo adafotokoza kuti amatsatira bwino ulangizi wa manyowa kutengera ndi mmene adaphunzitsiridwa choncho amapindula nawo.

“Ndi zoonadi kukachita ng’amba mbewu zanga sizifota msanga. Ndimakwanitsa kukonza ndi kuthira manyowa munda wanga onse ndisanafike mwezi wa October choncho mvula yobzalira ikagwa sindipanikizika ndimangoona zobzala basi,” adafotokoza motero.

Malingana ndi a Mpate, kathiridwe ka manyowa m’munda kamatengera kuchuluka kwa manyowa amene mlimi ali nawo.

Iwo adafotokoza kuti ngati mlimi ali ndi manyowa ochuluka, azithira manyowa m’khwawa lonse kapena kuti pakati pa mizere iwiri ndipo awakwirire akamapanga mizere yatsopano yobzalamo mbewu m’chaka chimenecho.

Ngati manyowa ndi ochepa, iwo adati mlimi ayambe wapanga mizere m’munda mwake ndi kukumba mapando obzalamo mbewu pa mlingo woyenera ndipo akatero athire manyowa m’mapandomo.

“Mvula ikagwa, mlimiyo amayenera adzabzale mbewu m’mapando momwe adathira manyowa,” adafotokoza motero.

A Mpate adaonjeza kuti kuchuluka kwa manyowa amene mlimi akuyenera kuthira m’munda kumatengera michere imene ili kale m’nthakamo choncho alimi amayenera kuyezetsa nthaka yawo.

Ngakhale izi zili chomwechi, iwo adati matani a manyowa osachepera 2.5 amafunika kuthira pa hekitala imodzi.

Related Articles

Back to top button
Translate »