Samalani ndi nyongolosi nthawi ya mvula ino
Kale alimi a m’gulu la ulimi wa ng’ombe la Chilangoma kwa mfumu yaikulu Kuntaja m’boma la Blantyre samapindula ndi ulimiwu kaamba ka tizirombo monga nyongolotsi ngakhalenso nkhupakupa makamaka nyengo ya mvula ngati ino.
Malingana ndi wapampando wa gululo, a Harry Zimpita, tiziromboti timapha kwambiri tiana komanso ng’ombe zambiri zazikulu zimaoneka zoonda ndi zonyentchera.
Tsopano ndi nkhambakamwa chifukwa mothandizidwa ndi alangizi alimiwa adapanga gulu limene padakalipano lili ndi alimi a ng’ombe za nyama oposa 90 ndi cholinga choti azitha kuthana ndi tiziromboti komanso matenda pamodzi.
“Patokha zimativuta chifukwa mankhwala ndi okwera mtengo koma alangizi athu atatitsegula m’maso ndi kumasonkherana ndalama zogulira ngati gulu kuti tizitha kutsatira ndondomeko yonse, ulimiwu udaphweka chifukwa zidayamba kuoneka za thanzi ndipo kufa kwa ana kudachepa,” adafotokoza motero.

Kupat u la kumwet sa mankhwala opha nyongolotsi, mlangizi wa m’deralo a Emmanuel Chikaonda adati adadzusanso dip thanki imene inkangokhala osagwira ntchito kuti azithana ndi nkhupakupa zimene zimasautsanso kwambiri ng’ombe makamaka m’dzinja.
Alangi z i a a ziweto m’boma amati nyongolosi ndi nkhupakupa zimaswana kwambiri mu nyengo ya mvula kaamba ka kuchuluka kwa chinyontho.
Chifukwa cha ichi, iwo amalangiza kuti alimi amayenera kupereka mankhwala opha nyongolosizi ku ziweto kumayambiriro kwa nyengo ya mvula ngati kuno ndi kumapeto kwa nyengoyi.
“Kumwetsa koyambiriraku kumathandiza kuti ziweto zipite m’nyengo ya mvula zilibe nyongolosi pamene kumwetsa kachiwiri kumathandiza kuti tichotse nyongolosi zonse zimene ziweto zatenga m’nyengo ya mvula.
“Izi sizikutipatsa malire opereka mankhwalawa ku ziweto chifukwa tikuyenera kuzipatsanso nthawi ina iliyonse ngati zagwidwa ndi tiziromboti,” adatero iwo.
Zina mwa zizindikiro zoonetsa kuti ziweto zagwidwa ndi tiziromboti ndi monga kutsegula m’mimba,kuimika ubweya, kuonda, kutupa kwa kunsi kwa khosi ndipo nthawi zina kutsokomola.
Kuonjezera apo, nyongolosizi zikachuluka zimatha kutseka matumbo ndipo mapeto ake chiweto chimafa.
Nyongolosi zina monga za nkhumba zimayenda m’thupi mwa munthu amene wadya nyama yosapsa ya chiwetochi mpaka kukafika ku ubongo. Mapeto ake munthu amatha kupenga misala.
Kawirikawiri izi zimachitika ziwetozi zikamadya m’malo monga m’madambo. Malo abwino ambiri odyetsera ziweto m’nyengoyi amakhala alimidwa choncho zimakadya ku dambo kumene kumapezeka kwambiri nkhono zimene zimanyamula nyongolotsizi.
Ziweto zikamadya udzu m’madambowa zimadyera limodzi ndi nkhono, choncho nyongolosi zimalowa m’chiwindi mwa ziweto.
Alimi akhoza kugwiritsa ntchito piperazine kumwetsa ziweto monga nkhumba ndi nkhuku pofuna kupha nyongolosizi pamene Ranox amagwiritsidwa ntchito kumwetsa ng’ombe ndi mbuzi.



