Chichewa

Maneb itulutsa maina aophunzira 10 okhoza kwambiri

Listen to this article

Bungwe la za mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) latulutsa mndandanda wa ophunzira 10 amene achita bwino kwambiri pa mayeso a Sitandade 8 a chaka cha 2023.

Malingana ndi chikalata chimene wasainira ndi mkulu wa bungwelo a Pulofesa Dorothy Nampota, msungwana wa ku sukulu yomwe si ya boma ya Playdor mu mzinda wa Blantyre, Alinafe Chulu, ndiye adaponderera ophunzira onse. Unduna wa maphunziro Lachiwiri udati ophunzira 267 330, omwe  136 751 mwa iwo adali asungwana, ndiwo adalemba mayesowo.

Otsatira Alinafe ndi anyamata atatu: Levison Henderson wa ku sukulu ya Nampeya ku Machinga, Angel Mbewe wa ku Mphongole ku Kasungu ndi Wakisa Ngosi wa ku Ekwendeni m’boma la Mzimba.

Alinafe Chulu

Polankhula nafe ku m’mawaku, Alinafe, yemwe ndi wa zaka 12, adati ndi wokondwa kuti wakhoza chotere.

“Ndine wokondwa kuti ndapambana chotere. Ndi Mulungu yekha amene walola kuti izi zikhale chomwechi. Ndikuthokoza makolo ndi aphunzitsi anga pondithandiza kuti ndichite bwino. Lidali khumbo langa akadandisankhira ku sukulu ya asungwana ya Lilongwe Girls, komabe popeza andisankhira ku sukulu ya sekondale ya Blantyre, sindingachitire mwina koma kukalimbikira basi,” adatero iye.

Malinga ndi chikalata cha Maneb, Patrick Mahoria wa ku Dzenje 2 ku Phalombe ndiye adali pa nambala 3 pomwe pa nambala 4 padali ophunzira anayi: Hastings Botha wa ku St Paul’s ku Mzimba, Gift Mwale wa ku Linga ku Nkhotakota, Cosmas Hamilton wa sukulu ya anyamata ya Guilleme ku Mchinji ndi Miracle Uka wa ku Sekeni ku Chikwawa. Pa nambala 5 pali Andrew Namalomba wa ku Chikale ku Nkhata Bay.

Mndandandawo ukudza pomwe undunawo udalengeza kuti Alinafe ndiye adakhazika pansi asungwana onse ndipo Levison adapuya anyamata pa mayesowo.  Mwa ophunzira 267 330 amene adalemba mayesowo, 234 645 adapambana ndipo mwa atsikana 136 751, opambana adali 116 195.

Related Articles

Back to top button
Translate »