ChichewaFront Page

Phindu lochuluka mu feteleza wa mkodzo 

Listen to this article

Ndi K12 000 yokha amagula feteleza wa mkodzo wokwana malita 20 ndi kusungunula n’kuthira m’munda.

Akatero mlimiyo a Winston Devie Banda amene amachita ulimi wa mvula ndi wa mthirira m’boma la Lilongwe amakhala athana nayo nkhani ya feteleza ndipo amangozisamalira kufikira zitacha koma zokolola zake zimakhala zofanana ndi zimene mlimi walima pogwiritsa ntchito feteleza wobereketsa ndi wokulitsa monga NPK, Urea ndi CAN.

“Ndikafuna kuti zipatso zikhale zazikulu kwambiri ndi zopatsa kaso koposa kuti ndikadye nazo bwino pa msika ndimathira kawiri koma kamodzi kamakhala kokwanira. Chiyambireni kugwiritsa ntchito fetelezayu chaka chatha m’mwezi wa January sindikhumbiranso kugula okwera mtengoyu,” adafotokoza motero.

Chinthu china choposa chimene adachipeza pogwiritsa ntchito feteleza wa mkodzo mlimiyu adati adazizimuka kuona kuti zilombo zina zimene zimamuzunguza ku ulimiwu monga zapansi zodula mbewu komanso za mtundu wa gulugufe sizipezeka pamalo pamene agwiritsa ntchito feteleza wa mkodzo.

A Samuel Jamuten a m’boma la Mchinji nawo amagwiritsa ntchito fetelezayu ku mbewu za m’dimba komanso za nthawi ya mvula zimene amalima monga tomato, tsabola ndi chimanga.

Iwo adafotokoza kuti padakali pano kuchita ulimi ngati bizinesi kukutheka ndi feteleza wa mkodzo chifukwa ndalama yogulira ndi yochepa kusiyana ndi feteleza winayu ndipo ntchito yake ndi yosalemetsa.

“Kuti bizinesi ipindule zolowa zimayenera zikhale zochepa kusiyana ndi zotuluka choncho kukwera mtengo kwa feteleza winayu kukuchititsa kuti zolowa zizichuluka kusiyana ndi zotuluka mapeto ake mlimi sapindula koma ndi feteleza wa mkodzo phindu likuchucha.

“Zaka za mmbuyomu fetelezayu timagula pa mtengo wa K4 000 ndipo tinkangokhala ngati sitikulowetsanso ndalama za feteleza,” adafotokoza motero.

Kusiyana ndi a Banda, a Jamuten adati amangothira kamodzi basi chifukwa akatero mbewu zidakali zazing’ono zimakula mpaka kubereka fetelezayu asadathe.

Iwo adamema alimi anzawo kuti ngati akufuna kupindula ndi ulimi m’nyengo ino pamene feteleza wochuluka akugulidwa pa mtengo wa K70 000 kupita m’mwamba pa thumba lililonse lolemera makilogalamu 50 abwere ku feteleza wa mikodzo sadzakhumudwa.

Malingana ndi bungwe limene likupanga komanso kupereka maphunziro kwa alimi ofuna kuphunzira kapangidwe ka fetelezayu la Evironmental Industries mogwirizana ndi sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) ndi bungwe la Center for Agriculture Transformation (CAT), mbewu zimachita bwino koposa mlimi akayambira kuthira manyowa m’munda asadabzale mbewu.

Mkulu wa bungwelo a Goodfellow Phiri adati fetelezayu amakhalitsa m’nthaka chifukwa ali mu gulu la feteleza wa chilengedwe choncho ndi wodalirika kusiyana ndi winayu.

“Kumbali ya zokolola, mlimi akalima mbewu pamunda wa nthaka monga wachionetsero umene tili nawo ku Luanar Bunda Campus mbewu zimene timalima pogwiritsa ntchito feteleza wa mkodzo wokha zimafanana ndi zimene mlimi walima pamalo a nthaka koma wagwiritsa ntchito NPK ndi CAN kapena Urea mwachitsanzo matumba opitilira 35 a chimanga olemera makilogalamu 50 pa ekala.

“Pamalo opanda nthaka zokolola za mbewu zimene zinalimidwa pogwirtsa ntchito feteleza wa mkodzo zimaposa za NPK ndi CAN kapena Urea,” adafotokoza motero.

Malingana ndi woona za nthaka ku nthambi ya kafukufuku wa zaulimi ya Bvumbwe m’boma la Thyolo a Peter Mfune, kafukufuku wa mkodzo adachitika ndipo adapeza kuti muli mchere wa Nitrogen umene ndi wofunika kwambiri ku mbewu.

Malingana ndi a Mfune, chidatsalira ndi kupeza kupeza kuchuluka kwa michereyi ndi kuchuluka kwa fetelezayu amene akuyenera kuthiridwa phando.

“Kolite ya mkodzo imatengera zakudya zimene munthu wadya ndi zinthu zina choncho kafukufuku akufunikabe kuti izi zidziwike,” iwo adatero.

Werengani pa tsamba 3 kuti mudziwe za mmene amapangira feteleza wa mkodzo komanso kagwiritsidwe ntchito kake.

Related Articles

Back to top button
Translate »