Chichewa

Umitsani chimanga mokwanira ngakhale mvula ikugwabe

Listen to this article

Adathawitsa chimanga m’munda chisadaumitsitse kuopetsa kuti chionongeka ndi mvula imene ikupitirirabe kugwa m’dziko muno komanso akuba amene akuba mopanda chisoni.

Mlimi wochokera m’boma la Blantyre a Margaret Chitani ndi alimi ena ochuluka a m’chigawo cha ku mmwera adali ndi chikhulupiriro kuti mvula idukizako ndipo akhala ndi mwayi wokachiyanika ku nyumba koma izi zakhala zovuta kwambiri chifukwa mvula nayo ikuoneka sikugonja koma chimanga chikuyenera chiume mokwanira chifukwa kupanda kutero chiola ndi kupanga chuku ngakhalenso kumera kumene.

Sabata ziwiri zapitazi kunja kumaoneka ngati kwa dzuwa koma zachisoni alimi amati akatulutsa mbewuyi kuti ayanike mvula imangoyamba mwadzidzidzi kuchititsa alimiwa kuchotsa mbewuyi mwansanga isadaume n’komwe?

“Tsiku lina chimanga chidanyowa ndithu chifukwa tidayanika chochuluka poona mmene dzuwa lidachitira koma chimvula chidangotsika nthawi imodzi mosayembekezeka.

“Kudali kovuta kuti mlimi uchotse zokolola zonse m’kanthawi kochepa choncho chinanyowa ndithu ndi kuchita matope moti timachita kutsuka,” adadandaula motero.

Osalola chimanga chiole ndi kuchita chuku

Malingana ndi katswiri wa za ulangizi wa za ulimi ku nthambi ya za maphunziro a za ulangizi ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) a Paul Fatch, pali njira zosiyanasiyana zimene alimi a m’maiko ena a mu Africa amagwiritsa ntchito kuumitsira mbewu zawo nyengo zikakhala zotere.

Iwo adati njirazi kawirikawiri sizigwiritsidwa ntchito m’dziko muno chifukwa nyengo imene ulimi wakumana nawo chaka chino sichitika kwambiri.

“Mwa zina, alimi m’maiko ena amakonza zipinda zouma bwino ndi zolowa ndi kutulutsa mpweya ndi kumwaza mbewu zawo mmenemo ndipo mbewu zimamalizika kuuma ndi mpweyawu.

“Ena amayatsa moto wa nkhuni m’zipinda zosungirazi kuti kutentha kochokera ku motowu kuthandize kuumitsa mbewu zawo,” adafotokoza motero.

A Fatch adaonjeza kuti maiko otukuka amagwiritsa ntchito nkhokwe zoumitsira mbewu zoyendera mphamvu ya magetsi kuumitsira mbewu zawo.

Iwo adati maiko ena alimi amamanga thandala ngati yoyanikira mbale koma yaikulu m’kitchini pamwamba pa malo ophikira ndi kusanjapo mbewu kuti kutentha kochokera ku moto kuziumitsa mbewuzo.

Wa zaulimi wa mbewu ku nthambi ya zakafukufufuku wa zaulimi ya Bvumbwe m’boma la Thyolo  a Frank Kaulembe adaonjezera kuti alimi akhoza kumanga mashedi oumitsira mbewu panja ngati mmene amachitira ndi mbewu ya fodya ndi kufolera bwino kuti mvula isamalowemo ndipo malo oyanikira akwezeko kuti mbewu zisamagunde pansi.

“Akuyenera kumazitembenuza pafupipafupi kuti ziziombedwa mphepo mbali zonse ndipo zimatha kuuma ndi mphepo.

“Pakapezeka mwayi wa dzuwa akhodza kumazitulutsa ndikuyanika pa dzuwa,” adafotokoza motero.

Iwo adachenjeza alimi kuti akuyenera kuumitsa chimanga chawo kufikira chinyontho chitachepa ndi 13 pelesenti kutsika m’munsi kuti akachisunga m’matumba chisaole ndi kuchita chuku.

Kuti mlimi adziwe ngati mbewuyi yafika apa, a Kaulembe adati akachitenga ndi kumathira m’thumba kapena kuchiponya chimachita phokoso.

Njira ina iwo adati mlimi akhodza kuluma mbewu imodzi ndi mano ndipo ngati yamveke kuti kha! Posweka ndiyekuti yauma koma ngati yangogamphuka imakhala sidaume.

“Njira ina alimi  amene ali ndikuthekera kotengako mbewu zawo zochepa n’kupita nazo ku malo a kafukufuku wa za ulimi kuti akayezetse chinyonthochi akhoza kutero,” adafotokoza motero.

Related Articles

Back to top button
Translate »