Kwin Bee: Kulimbikitsa ufulu wa atsikana

Atsikana oimba chamba cha Afro ndi hip hop alipo ndithu m’dziko muno, koma munthu wotchula mndandandawu amayenera kusololetsa milomo yake chifukwa muli Kwin Bee. Uyu ndi mtsikana yemwe watchuka ndipo wavekedwa chisoti chomenyera ufulu akazi kutsatira nyimbo ya Ndadutsa Pompo yomwe adaimba ndi anzake. Nyimboyi imayankha mwano wa anyamata kwa atsikana womwe uli mu Wadutsa Pompa ya W-Twice mothandizana ndi Nepman. TEMWA MHONE adakumana ndi mtsikanayu ndipo adacheza motere:

Kwin Bee: Ndikulingalira
zokhazikitsa chimbale

Kwin Bee, tikudziwe?

Ine ndi Bertha MacDonald Lomoti wochokera m’mudzi mwa Suweni kwa T/A Chapananga m’boma la Chikwawa. Ndine m’Mang’anja ndithu ndipo ndimakhalira kwa Manase mumzinda wa Blantyre. Dzina la Kwin Bee sichidule cha Bertha, koma likuchokera pa mtundu wa njuchi zobereka (queen bee). Izi ndi kholo la njuchi ndipo limatanthauza kuti moyo umakhala ndi zopinga zomwe munthu amayenera kugonjetsa kuti adye malesa kapena uchi. Pokhala woimba, ndimawonetsetsa kuti uthenga uzikhudza okonda luso langa m’magawo amenewo.

Kuimba udayamba liti?

Ndidayamba ndili ndi zaka zitatu zakubadwa chifukwa chachilimbikitso cha MacDonald Lomoti. Awa ndi bambo anga omwe amadziwa luso lamaimbidwe. Chachikulu ndi choti ndimaimba chifukwa ndimakonda nyimbo.

Kodi uthenga m’nyimbo zako ndi wotani?

Kulimbikitsa akazi kudzidalira komanso kumenyera ufulu wa anthu. Sindimakondwa kuona wina akuponderezedwa kaamba kokhala mkazi.

Udayamba pakale, koma yowinira ku mtundu wonse idali iti?

Nyimbo ya Nd’zakudandaula Chikadzatha yomwe ndidatulutsa mu 2014 ndi imene idandifikitsa m’makomo ndi m’mapwando a anthu. Nyimboyi ndimene ndikupangira ndalama kwambiri pakadalipano. Baba, ndiye Amalawi ayembekezere nyimbo ina ya nyatwa yomwe ndikuti Achisale.

 

Umakhalira kuimba basi?

Ayi. Ndimagwira ntchito kukanema ndi wailesi za Angaliba ngati muulutsi komanso mkonzi. Kupatura zimenezi, ndimalimbikitsanso atsikana kukwaniritsa masomphenya awo pansi pabungwe la Youth Net and Counselling (Yoneco). Ndilinso ndi ka bizinezi kena nanga ndizichita kusowa yophodera.

Omvera amafuna chimbale, Kwin Bee achitulutsa liti chake?

Ndikulingalira zochikhazikitsa chaka cha mawa, koma mu November chaka chino ndikhazikitsa nyimbo zanga zitatu, zomvera ndi mavidiyo. Adekhe ndithu ndiwavinitsa.

Ndiwe mmodzi mwa atsikana othwanima pamaimbidwe amakono m’dziko muno, chinsinsi chili pati?

Ndimayamba kuchita zinthu ndi zochepa zomwe zilipo. Kutulutsa zothyakukaku ndi chifukwa cha chidwi ndi nthawi yokwanira yolemba nyimbo zoti anthu azizikonda. Komanso sindikopera kuimba ndipo ndimachita ngati Kwin Bee zomwe zikutukula luso langa.

Ntchito yomenyera ufuluyi ukuyichita motani?

Aliyense adziwe kuti zinthu zimachitika ndi cholinga m’moyo. Uthenga ndi woti kulakwitsa kusamulepheretse munthu kukwaniritsa maloto ake owala ngakhale angachedwe azafika basi. Kudzera munyimbozi, omvera amadziwa zochita malingana ndi nyengo akudutsamo.

Mawu kwa okonda nyimbo?

Amalawi adandilandira ndiye apitirize chifukwa zabwino zikubwera komanso Mulungu aziwadalitsa. Padakalipano ndikufuna munthu wotukula luso langali. n

 

Share This Post