Chichewa

Lutepo wakundende

Listen to this article

lutepo

Bwalo lalikulu la milandu ku Zomba (High Court) Lachisanu lapitali lalamula Auswald Lutepo, yemwe ndi mmodzi mwa anthu omwe akuyankha milandu yokhudza kusolola ndalama za boma wotchedwa kuti Cashgate, kuti akakhale m’ndende kwa zaka 11 popezeka wolakwa pamlanduwu. Popereka chilango, jaji Redson Kapindu adati pamlandu woyamba wopanga upo pofuna kubera boma, Lutepo akaseweze zaka zitatu ndipo wachiwiri, wosolola ndalama zokwana K4.2 biliyoni, akaseweze zaka 8. Zilango zonsezi ziyendera limodzi kuyambira pa 11 June pomwe iye adapezeka wolakwa pamilandu yonse iwiri. Jajiyu adati wamumverako chisoni pamplandu wachiwiri kaamba koti adabwezako ndalama zokwana K370 miliyoni. –Joseph-Claude Simwaka

Related Articles

Back to top button
Translate »