Chichewa

Kuchitsedwa ntchito ndi zina

Listen to this article

Mourinhao ndi mmodzi mwa anzanga amene ndimacheza nawo pa Wenela. Sindikudziwa kuti nchifukwa chiyani mkuluyu amakonda Arsenal. Momwe amaonekera, nzeru zake, ndimadabwa kuti iyeyu ndi Arsene Wenger adadyetsana mankhwala a mtundu wanji.
Nchifukwa chake nthawi zambiri tikamukumbutsa kuti patha zaka 10 timu yakeyo isanachite zakupsa potenga chikho amakwiya zedi! Koma iyo ndi nkhani ya tsiku lina.
Tsono Mourinhao adatopa ndi kuitanira minibasi, ndipo adapempha mwini minibasi ina kuti amupezere ntchito. Mwini minibasiyo adali dotolo. Pambali pothandiza odwala ku Gulupu, dotoloyo amakaphunzitsanso kusukulu ina ya anamwino.
“Apa zili bwino Tade. Kukhosi kwanga kuchita kusalala. Bakhalani ndi kuitanira kwanuko mpaka day yobwera Yesu. Uku kukumakhala kudya za tswayitswayi osati masewera,” adandiuza tsiku lina atatizungulira pa Wenela.
Koma ngati adathako sabata zitatu? Ndidangoona akubwera tsiku lina atazyolika.
“Bwanjinso nanga?” ndidamufunsa.
“Ndailephera ntchito. Andichotsa,” adayankha mwa chidula.
Apa mpomwe adafotokoza momwe ntchitoyo idathera.
“Ndimagwiranso ntchito yokonza m’nyumba mwa dotoloyo: kukolopa, kusesa, kukonza mufiliji ndi zina zotero. Tsiku lina, ndidapeza kuti liver ina idakhalitsa m’filijimo. Ndidaaitenga kukaotcha kunyumba. Atabwera mkulu uja adandifunsa: ‘Ndinasiya katundu umu, watenga ndani?’ Ndipo ndidati sindikudziwa,” adafotokoza mkulu uja.
Adamezera malovu, nkupitiriza: “Nthawi ya nkhomaliro adandifun-sanso, ndidakananso. Ngakhalenso madzulo adandifunsa ngati ndidaona katundu wake, ndidakananso. Pobwera madzulo tsiku linalo, adabwera ndi mowa umene adandigaila.”
Akuti mkuluyo ataona kuti Mourinhao wayamba kuledzera adamufunsanso: “Ndinasiya katundu wanga. Watenga ndani?” Ndipo Mourinhao adayankha: “Mukunena nyama ija? Ndaotchera, pepani.”
Mkulu uja adangoti: “Chinalitu chiwindi cha munthu ndimati ndikaphu-nzitsire.”
Abale anzanga, tikakhala pantchito sib wino kusolola ngakhale zimene tikuziona kuti nzazing’ono. Tikadakhala kuti tonse tilibe mtima osolola, nkhani ngati zotengera abale ndi alongo kunja moononga ndalama, kubwereka ndege yaufiti ngati kabanza si bwenzi zikutisautsa.
“Hallo Tade, wasowatu. Ndalanga wina uku,” adatero Abiti Patuma, msungwana wosowa ngati Adona Hilida pano pa Wenela.
“Zinakhalanso bwanji?” adafunsa Gervazzio, mmalo moika nyimbo ya Nakulenga.
“Amakula mtima, ati mkazi wake amamukhulupirira koopsa ndipo iyeyo kanali koyamba kuti apusitse mkazi wakeyo pocheza ndi ine. Poti anali ataledzera modziiwala, ndinatenga mapepala onse amagwiritsa ntchito nkuwaika m’thumba la buluku,” adatero Abiti Patuma.
Adaonjeza kuti mawa lake, adangomva kuti ukwati wamkuluyo watha.
Zoona, pamene tikulira pano pa Wenela, monga adachitira mkulu wina woona za maula, sibwino kutaya nthawi ndi zopanda pake. Inde, Moya Pete wakwiya, ndipo wati saleka kuyenda, koma abale anzanga, samalani. Pajatu wopita kumdulidwe sakwera njinga!
Gwira bango upita ndi madzi!

Related Articles

Back to top button
Translate »