Chichewa

Za kulephereka kwa zisankho

Listen to this article

Muzina

Edi mwana

Edi sebe santu

Muzina zizata mfana

Ya muzina

Sindikudziwa ngati Papa Wemba nyimboyo adaimverapo koma ndimo ndinkayimvera pamene inkaphulika malo aja timakonda pa Wenela. Gervazzio ndiye adaika nyimboyo pokumbukira Papa Wemba amene watsikira kwachete.

Koma dziko ili! Zoona likutenga anthu ofunika ndi otchuka, achina Prince, kusiya ife ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela. Imfa ikusiya zilengwalengwa.

Tsiku lina ndidzaipha imfa yotenga mayi kusiya mwana akulira.

Tsikulo wina adati ndipite ndikaitanire ku Mibawa. Koma nkadadziwa kuti amandikankhira kunkhondo!

art

Padafika asirikali atavala nkhwani-nkhwani. Komatu eni minibasi samaimva, ati khobwe akatolera kuti? Nawo adabwera ndi mapanza awo, inde magigo.

“Sitiimva. Minibasizi ndi zanu kuti muzitolera ndalama?” adatero phanza wina, atanyamula miyala.

“Kupanda nzeru. Malowa ndi anu? Kodi ogulitsa nkhwani mumsika angamemane kuti azitolera ziphaso ndiwo chifukwa nkhwaniwo ndi wawo? Kupusa! M’nyumba ya mwini saotchera mbewa,” adatero wapolisi wina, akukanyanga mmodzi mwa magigowo n’kumuponya m’chimbaula adachilawa Chihana.

Apo ndeu idabuka koma paja lamulo liposa mphamvu, akhonsolo adawina ndipo adayamba kutolera ndalama kuchokera kwa madalaivala.

Nditabwerera ku Wenela, ndidapeza Abiti Patuma ndi ena onse akumvetsera wailesi.

“Chisankho chimati chikhalepo ku Mchinji chalephereka. Boma silidapereke ndalama ati chifukwa lilibe,” adatero muulutsi.

“Boma lilibe ndalama bwanji? Koma chisankho cha ku Zomba ndiye adapeza ndalama? Pafa khoswe apa,” adatero Abiti Patuma.

“Paja nawe, kumangomva fungo la khoswe paliponse? Kulitu njala uku,” adatero bambo amene adali naye tsikulo.

“Zanu. Komabe inetu ndikuona kuti Dizilo Petulo Palibe ikuona kuti kuchititsa chisankho ku Mchinji kukhoza kuchititsa Male Chauvinist Pigs kuoneka mashasha,” adayankha Abiti Patuma.

Abale anzanga, musandifunse amatanthauzanji chifukwa nane sindikudziwa. Pajatu ine za matchera ayi.

“Padakalipano boma likuphwanya malamulo omwe amaneneratu kuti chisankho chiyenera kuchitika pasanathe masiku mwakuti,” adatero Abiti Patuma.

“Mukutayatu nthawi. Paja zomatiuza kuti chakuti chichitike pofika tsiku lakuti si mbali yathu,” adatero bambo adali naye uja.

“Mukutanthauza kuti nthawi yokhala pampando ikadzatha, Mustafa sadzafuna kubweza mpando kwa Ajibu?”

Adangoti duuu mkulu uja. Adalandira foni.

“Mwati bwanji? Shati Choyamba watisiya? Zabodza izo, nkadamva. Ndikudziwa kuti ali ku Tajkstan komwe amuchotsa dzino dzana. Kukonda kupekera ena imfa bwanji? Akukupanitu makofi akabwera,” adatero mkuluyo adatero.

Imeneyinso idandipita. Malingaliro adali kwa Papa Wemba komanso Prince.

Gwira bango iwe! Upita ndi madzi!!! n

Related Articles

Back to top button
Translate »