‘Bweretsani zakudya osati Sim-card ku ndende’
Mkulu wa asilikali pa ndende ya Zomba Central Prison a Austin Nyoni ati m’malo mowotcha kapena kuphwanya ma foni ndima sim-card opezeka ndi akayidi pa ndendeyo ati azipititsa zinthuzo ku kampani za lamya kukasaka eni aziphaso zimene adalembetsera fonizo.
Malinga ndi a Nyoni, ati eni ziphasozo akapezeka azigwidwa ndi kuyimbidwa mulandu olowetsa zinthu zoletsedwa mu ndende zimene ati zikukolezera umbava kudzera pa foni mdziko muno.

Iwo anena zimenezo potsatira chipikisheni cha mafoni ndima sim card chimene chidachitika Lolemba sabata ino pa ndendeyo.
“Zimene zidalandidwazo eni ziphaso za zipangizozo akadziwika azisakidwa ndikugwidwa kukayankha mulandu,” atero iwo.
A Nyoni ati kupatula kubedwa kwa ndalama ati mafoniwo ali ndi kuthekera kokhwefula chitetezo pa ndendeyo.
“Kunoko muzibweretsa chakudya osati ma foni ndi sim-card chifukwa mukagwidwa lamulo lidzagwira ntchito pa inu,” atero iwo.
Iwo adawunikira kuti ntchito yosintha akayidi siya asilikali okha a ndende koma ya dziko lonse makamaka anthu amene ali ndi abale awo kapena a mnzawo mu ndendemo.
“Pamene mukulowetsa ma foni ndi sim-card mumachititsa kuti m’malo mosintha anthuwa mumakhala mukukolezera moto kuti azipitiliza kuchitabe umbava ndi umbanda,” adatero iwo.
A Maxwell Aubi ndi a Esther Kabudula a m’bomalo ati ganizo lomanga eni ziphaso za zipangizozo ndi loyenera.
Malinga ndi a Aubi ndalama zimene anthu amaberedwa ndi anthu apa ndendeyo ndi ndalama zimene oberedwawo akadakwanitsa kupangira chitukuko cha mabanja awo ndi dziko lawo.
“Tigwirane manja ndi a ndende posintha akayidi osati kukolezeranso kuti anthuwo azibabe,” atero iwo.



