Achinyamata akufuna maudindo
Mtsogoleri wa bungwe la Youth and Society a Charles Kajoloweka asindika kufunika kokhazikitsa malamulo okakamiza boma kuti lizipereka maudindo ena akuluakulu kwa achinyamata.
Iwo alankhula izi Lachitatu mu mzinda Lilongwe komwe achinyamata amakhazikitsa manifesito yawo n’cholinga choti yiunikire atsogoleri ndi zipani za ndale pamene zikukonza ma manifesito awo a zisankho za pa 16 Sepitembala.
Iwo adati malamulo a dziko lino amateteza ufulu wa amayi ndi anthu aulumali, koma safotokoza molunjika zokhudza achinyamata.

“Padakali pano tilibe malamulo, mwachitsanzo, okakamiza boma kuti mwa maudindo 100 alionse 30 azipite kwa achinyamata.
“Manifesito ya achinyamata ndi mlozo womwe mtsogoleri wa dziko lino yemwe timusankhe pa zisankho za pa 16 Sepitembala adzagwiritse ntchito posankha maunduna, komanso anthu otsogolerera madipatimenti ndi mabungwe aboma,” adatero a Kajoloweka.
Iwo adati bungwe lawo ligwiritsa ntchito manifesitoyo pokhambirana ndi atsogoleri a ndale omwe akufuna kuti achinyamata adzawavotere pa zisankho zikudzazi.
Pothirirapo ndemanga, mkulu wa bungwe la United Nations m’dziko muno a Rebeccah Ada Donto adati kupereka mphamvu kwa achinyamata n’koyenera potengera ndi chiwerengero chawo.
“Koma msonkhanowu sukuunika za chiwerengero cha achinyamata chokha, komanso za ufulu ndi kuthekera kwawo,” iwo adatero.
Ada Donto adati achinyamata si atsogoleri amawa okha, komanso a lero.
“Achinyamata ali ndi maluso komanso kuthekera kugwira ntchito zosiyanasiyana zotukula dziko lino,” iwo adatero.
A Mwandida Theu, mmodzi mwa akuluakulu a kampeni ya Youth Decide, adapempha atsogoleri andale kuti awerenge manifesitoyo kuti adziwe zomwe achinyamata a m’dziko muno akufuna ndi kuzilingalira kwambiri popanga ma manifesito a zipani zawo.
“Mwa anthu 100 alionse omwe ali m’dziko muno, 60 ndi achinyamata. Kuphatikizira apo, kaundula wa zisankho akuonetsa kuti mwa anthu 100 alionse omwe adalembetsa, 63 ndi achinyamata.
“Choncho achinyamata akuyenera kutenga gawo lalikulu m’zipani, m’madipatimenti, maunduna ndi mabungwe a boma kuti dziko lino lipite patsogolo,” iwo adatero.
Sipikala wa Nyumba ya Malamulo, a Catherine Gotani Hara adapempha achinyamata kuti achilimike pomenyera ufulu wawo.
“Musatope, musabwerere mmbuyo pomenyera ufulu wanu. Aphungu akangosankhidwa, akumbutseni zomwe mukufuna.
“Ndanena izi chifukwa mmene timatsiriza kukumana kwathu kwa Nyumba ya Malamulo palibe phungu amene adatulutsa nkhani yokhudza achinyamata.
“Ichi n’chifukwa sitidakambirane zokhudza achinyamata,” iwo adatero