National News

Ulendo wa a Kondowe pa ndale

Phungu wa Nyumba ya Malamulo wa dera la kumpoto cha kumvuma kwa boma la Nkhotakota a Overstone Kondowe akuti ulendo wawo pa ndale udali wozuna ndipo alimbikitsa anthu aulumali ambiri kuti adzapikisane nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala.

Iwo auza nyuzipepala ya 2025 Ndi Ifeyo kuti nthawi yomwe akhala m’Nyumba ya Malamulo yawasimikiza kuti palibe kusiyana pakati pa munthu waulumali ndi walungalunga pa ndale.

A Kondowe ndi munthu woyamba wa chialubino kukhala phungu wa Nyumba ya Malamulo m’mbiri ya dziko lino.

Mkuluyu adasankhidwa kukhala phungu nthawi yamikwingwirima yomwe anthu achialubino amadulidwa ziwalo, komanso kuphedwa m’dziko muno.

Kondowe: Munthu
wa aulumali ali
ndi kuthekera

“Mavuto omwe anthu achialubino amakumana nazo sanandibwezere m’mbuyo, koma adandipatsa mangolomera woima ngati phungu.

“M’nyumba ya Malamulo ndakhala ndikulankhula kwambiri za anthu aulumali makamaka mavuto omwe amakumana nawo, kuthekera kwawo, komanso zomwe boma lingachite pofuna kuthana ndi mavuto awo,” atero a Kondowe.

Iwo afotokoza kuti kusankhidwa kwawo kukhala phungu ndi umboni woti anthu aulumali ali ndi kuthekera ngati munthu wina aliyense.

A Kondowe akuti ubale wawo ndi aphungu achipani chawo cha Malawi Congress Party (MCP), komanso a zipani zotsutsa boma uli bwino kwambiri.

“Aphungu anzanga amanditenga ngati wina aliyense. Timacheza opanda kusalidwa kapena kulankhulidwa mawu achipongwe,” afotokoza choncho phunguyu.

A Kondowe adasankhidwa mu 2021 potsatira imfa ya yemwe adali phungu wa deralo a Martha Lunji.

“Zitukuko zomwe a Lunji adasiya ndapitiriza ndi kutsiriza chifukwa zinali zofunika kwambiri kwa anthu a m’deralo.

“Anthu a ku Bua mpaka ku Dwangwa analibe madzi a m’mipope kupatula a pa Misson ya Luwalazi, koma padakali pano akumwa madzi aukhondo.

“M’dera langa ndikulimbikitsa ntchito zaulimi ndi za usodzi popeza anthu ambiri ndi asodzi ndi alimi,” iwo atero.

Mu nthawi yawo ngati phungu, a Kondowe akuti akhazikitsa malo owonjezera ogulitsirako zipangizo zaulimi zotsika mtengo, akhazikitsa khoti pa Luwalazi, kumanga misika pa Chisenjere ndi Chamlame.

Iwo apempha anthu a m’deralo kuti awavoterenso kaamba koti akufuna agwirizane ndi boma poitanitsa makampani kuti adzayambitse ntchito za migodi m’deralo.

“Mogwirizana ndi aphungu anzanga tikufuna Nyumba ya Malamulo ikadutsitse lamulo lokhudza ulimi wa nzimbe ndi malonda a shuga chifukwa anthu a m’dera lino amalima kwambiri nzimbe.

“Likadzadutsa lamuloli, miyoyo ya anthu ambiri a m’dera lino idzatukuka. Kuyambira kalekale ulimi wa chamba umachita bwino m’boma lino. Choncho ndikabwerera ku Nyumba ya Malamulo ndidzayetsetsa kuulimbikitsa,” atero a Kondowe.

Pothirirapo ndemanga, mkulu wa bungwe la Association of Persons with Albinism (APAM) a Maynard Zachariah ayamikira a Kondowe kaamba koimirira bwino anthu a m’dera lawo komanso anthu aulumali a m’dziko muno.

“A Kondowe si kuti ayimirira bwino anthu a m’dera mwawo mokha ayi, komanso anthu aulumali a m’dziko muno.

“Ndiyam-ikirenso anthu a m’dera la kumpoto chakumvuma kwa boma la Nkhota-kota kaamba kopereka mwayi woti munthu wa chialubino awayimirire,” iwo atero.

A Zachariah akuti a Kondowe awonetsa kuti munthu waulumali atha kugwira ntchito yomwe walungalunga angagwire.

Iwo alimbikitsa anthu aulumali omwe akufuna kudzaimira kuti asagwe mphwayi, koma apikisane nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala.

Anthu aulumali omwe akufuna kudzaima nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala akuti a Overstone Kondowe, Clement Terence Chiwaya, Susan Chitimbe ndi George Claver ndiwo amawapatsa mangolomera ofuna kuimira madera awo.

A Emilia Chapaheya, womwe akudzaimira ngati phungu m’dera la kummwera chakumvuma kwa boma la Mulanje, afotokoza kuti ndale za a Chiwaya, Kondowe, Chitimbe ndi a Claver ndizo zidawalimbitsa mtima kuti atha kukwanitsa ndale.

“Anzathu adaimira madera awo ndipo adachita bwino kwambiri. Ichi ndi chilimbikitso chachikulu pa moyo wanga,” adatero mayiwa womwe sakukaika kuti adzachita bwino.

A Umali Sungani, womwe akudzaimira ngati khansala ku Sankhwi ndi Mphamvu Kalima omwe akudzaimira ngati khansala m’dera la Nyamadzele ku Nsanje akuti ndale za a Chiwaya, komanso a Kondowe zimawasuntha kwambiri.

“Anthu amenewa amandilimbitsa mtima,” atero a Sungani womwe akukhulupirira kuti adzachita bwino.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button