Akhazikitsa ndondomeko zoletsaandale kukopa ovota ndi katundu
Mkulu wa ofesi yoona m’mene zipani za ndale zimagwirira ntchito zawo, a Kizito Tenthani, akhala akukumana ndi atsogoleri a zipani za ndale komanso kuchititsa misonkhano n’cholinga choti Amalawi adziwe m’mene ndondomeko zoletsa andale kukopa ovota ndi ndalama komanso katundu zizigwirira ntchito.
Ofesi ya a Tenthani imalephera kugwiritsa ntchito lamulo loona za zipani kaamba koti idalibe ndondomeko.
Ndondomekozo adazisindikiza pa 23 Meyi patangotsala mwezi umodzi kuti bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) litsegulire nyengo yochititsa misonkhano yokopa anthu.

A Kizito adati ndondomekozo zikusonyeza kudzipereka kwa boma pofuna kuthana ndi mchitidwe wokopa ovuta ndi ndalama komanso katundu.
“Tikukumana ndi atsogoleri a ndale kuti adziwe za ndondomekozi ndi zimene tikuwayembekezera,” iwo adatero.
Lamulo loona za zipani limalola andale kupereka zovala za makaka a chipani chawo, zakudya komanso ndalama zoyendera kwa owatsatira.
Koma lamulo silikulola andale kupereka ndalama, katundu kapena mphatso zomwe cholinga chake ndi kukopa kapena kukakamiza anthu kuti awavotere pa zisankho.
Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) Trust a Gray Kalindekafe apempha
(WOLREC).
Poyankha nkhaniyi mlembi wa chipani cholamula cha Malawi Congress Party (MCP) a Richard Chimwendo Banda, mu progalamu ya Mulimba, adati chipani chawo chikutsatira zomwe adasayinirana moti chidatsitsa ndi theka ndalama zomwe amayi amayenera kupereka kuti apikitsane nawo pa zisankho zachipulula.
“Mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus Chakwera amatsatira ndondomeko ya boma yoti mwa maudindo 40 pa 100 iliyonse azipita kwa amayi pamene abambo azitenga maudindo 60 pa 100 iliyonse.
“MCP ikuchita izi kuyambira posankha maunduna, komanso m’maudindo ake m’chipani.
“MCP ndi chipani chokhacho chomwe chili ndi amayi awiri omwe akutsatira kwa mtsogoleri wake a Lazarus Chakwera.
“A Abida Mia ndi wachiwiri kwa a Chakwera m’chigawo chakummwera pamene m’chigawo cha ku mpoto a Kizito kuti agwiritse ntchito ndondomekozo mosayang’ana nkhope.
Pothirirapo ndemanga pa nkhaniyi, mtsogoleri wa amayi a ndale m’dziko muno a Mary Thom Navicha akuti ndi wokondwa kuti tsopano ndondomekozo ziyamba kugwira ntchito.
“Ndine wokondwa kaamba koti amayi, achinyamata ndi anthu ena aulumali anali omangika kuchititsa misonkhano kaamba kosowa ndalama zopereka kwa anthu m’misonkhano yawo,” iwo atero.
Mneneri wa chipani cha Alliance for Democracy a Linda Limbe akuti ndondomekozo zithandiza kuchepetsa mavuto omwe andale amakumana nawo.
A Juliana Pasani a m’boma la Mulanje, a Joseph Zakariah a ku Dedza, Silvester Njikho a ku Nsanje, a Ganizani Mhango a ku Rumphi adati vuto ndi atsogoleri a ndale kaamba koti amangofuna kugwiritsa anzawo ntchito nthawi ya chisankho.
“Andalewa tikawaika m’mipando amatithawira n’kukakhala ku Blantyre kapena Lilongwe kutisiya ife manja ali mkhosi. Choncho timafuna tidyeratu zathu nanga si timawathandiza kuti alemere,” atero a Pasani.
Mabungwe a Oxfam ndi Women Legal Resource Centre (WOLREC) akhala akulimbana ndi mchitidwe wokopa anthu ndi ndalama komanso katundu kaamba koti umachititsa kuti amayi ambiri asapeze mipando.
“Ndale zokopa anthu ndi ndalama komanso katundu ndizo zikubwezera mmbuyo ntchito yoti pasakhale kusiyana pakati pa abambo ndi amayi pa ndale.
“Tikaunika tipeza kuti ndale zoterezi zimakomera abambo kaamba koti ndiwo amakhala ndi ndalama zokopera anthu poyerekeza ndi amayi, achinyamata ndi anthu aulumali,” atero mkulu wa Oxfam a Lingalireni Mihowa.
A Emilia Chapaheya, womwe akudzaimira ngati phungu m’dera la kummwera chakumvuma kwa boma la Mulanje, agwirizana ndi a bungwe la Oxfam ndi WOLREC.
“N’zoona ndalama zikumavuta,” iwo atero.



