Mafumu akulimbikitsa amayi
AYAMBA KANDODO NDI BRIGHT KUMWENDA
Mafumu akufuna amayi, achinyamata ndi anthu aulumali ambiri atenge nawo gawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala.
Polankhula ndi nyuzipepala ya 2025 Ndi Ifeyo, a mfumu a Chowe a ku Mangochi alonjeza kuti apempha nyakwawa ndi mafumu onse a m’bomalo kuti alimbikitse amayi, achinyamata ndi anthu aulumali kudzaima nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembara.
A Victoria Kingstone, omwe akufuna kudzaimira dera lapakati pa boma la Mangochi, adauza msonkhano womwe bungwe la Civil Society Strengthening (CCSS) lidachititsa m’bomalo kuti anthu ena akutukwana ndi kulankhulira mawu achipongwe amayi.
“Izi zimabwezera mmbuyo maloto athu pa ndale ndi kugwetsa mphwayi amayi ambiri omwe akufuna kulowa ndale,” iwo atero.
Pothirirapo ndemanga, a Chowe akuti n’zomvetsa chisoni kuti amayi omwe akufuna kupikitsana nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala akukumana ndi mikwingwirima ndipo adaopseza kuti athana ndi aliyense wochita izi.

“Ndikumana ndi mafumu komanso nyakwawa zanga kuti akhale tcheru ndi kupereka chindapusa kwa aliyense wochitira amayi mtopola m’madera mwawo,” alonjeza choncho a mfumuwo.
A mfumu a Kachindamoto a m’boma la Dedza ndi a mfumu a Kameme a m’boma la Karonga adzudzula anthu omwe akuchitira amayi ndi anthu aulumali mtopola.
“M’dera langa lino ndidawauziratu kuti amayi ndi anthu aulumali ali ndi ufulu wopikisana pa mpando uliwonse wa ndale ndipo sindikufuna wina kuwatukwana kapena kuwachita chipongwe,” atero a Kachindamoto.
Nawo a mfumu a Chikulamayembe a m’boma la Rumphi akuti ndi ufulu wa amayi, achinyamata ndi anthu aulumali kuchita nawo ndale.
“Sindidzalola aliyense kuphwanya ufulu wa amayi, achinyamata ndi anthu aulumali m’dera langa,” iwo adatero.
A mfumu Jalavikuba a m’boma la Mzimba ndi a mfumu a Kameme a m’boma la Karonga alimbikitsa amayi kutenga nawo gawo pa ndale.
“Abambo tawayetsa, koma taona tokha kuti zikuwakanika. Choncho ndi nthawi yoti amayi akhale ndi mwayi wotenga gawo pa ndale,” iwo adatero.
Katswiri wa za ndale wa ku sukulu yaukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS) a Chimwemwe Tsitsi apempha mafumu kuti agwirane manja ndi zipani za ndale kuti chiwerengero cha amayi chikwere m’Nyumba ya Malamulo.
Mwa aphungu 193 omwe ali m’Nyumba ya Malawi aphungu 40 okha ndi amayi.



