A Joyce Banda ndi amayi okhawo omwe akufuna kudzapikisana nawo
Pofika dzuro m’mawa, atsogoleri 14 ndiwo anatenga makalata kuchokera ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) ofuna kudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino.
Chiwerengero cha onse omwe atenga kale makalata ndipo akufuna kudzayima ngati aphungu ndi makhansala sichikudziwika, malingana ndi mneneri wa bungwelo a Sangwani Mwafulirwa.
Padakali pano mtsogoleri wa dziko lino komanso wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Lazarus Chakwera ndi a Peter Mutharika a Democratic Progressive Party (DPP) adatenga kale makalata awo.

Atsogoleri ena omwe atenganso makalata awo ndi a Joyce Banda a People’s Party, a Atupele Muluzi a United Democratic Party, a Dalitso Kabambe a UTM, a Kamuzu Chibambo a People’s Transformation Party, a Frank Mwenifumbo a National Development Party, a David Mbewe a Liberation for Economic Freedom Party, a Kondwani Nankhumwa a People’s Development Party, komanso a Kwame Bandawe a chipani cha Anyamata, Atsikana, Amayi.
A Milward Tobias, Hardwick Kaliya, Adil Chilungo ndi a Smart Swira adzaima paokha pa chisankhochi.
Padakali pano a Joyce Banda ndi mayi yekhayo yemwe akufuna kudzapikisana nawo pa chisankhozi cha mtsogoleri wa dziko lino.
Pothirirapo ndemanga, katswiri wa ndale wa ku Malawi University of Business and Applied Sciences a Chimwemwe Tsitsi wati zomwe zikuchitika m’dziko muno sizachilendo.
“Ngakhale m’maiko a ku Ulaya si amayi ambiri omwe amapikisana nawo pa mpando wa pulezidenti,” iwo atero.
Katswiriyu akuti m’boma la demokalase zipani za ndale ndizo gwero la maudindo onse.
“Dziko la Malawi limatsatira boma la demokalase lomwe limapereka mphamvu kwa osatira zipani, kudzera m’misonkhana yawo ikuluikulu, kusankha atsogoleri omwe akufuna adzawayimire pa chisankho cha pulezidenti monga chomwe tikhale nacho pa 16 Sepitembala.
“Choncho amayi ayenera kupatsidwa mpata wopikisana nawo m’maudindo akuluakulu kuphatikizirapo woimira zipani zawo ngati pulezidenti wa dziko,” atero a Tsitsi.
Akuluakulu a zipani za MCP, DPP ndi UTM, omwe sadafune kutchulidwa maina, akuti sakudziwa anthu omwe adzaimire limodzi ndi atsogoleri awo (runningmates).
Wapampando wa MEC a Annabel Mtalimanja apempha aliyense yemwe akufuna kudzachita nawo zisankhozi kuti alipiriretu asadatenge makalata ku bungwe lawo. “Ndikudziwitsa zipani za ndale ndi anthu omwe akufuna kudzaima pa mipando yosiyanasiyana kuti MEC yaonjezera nthawi yopereka makalata” iwo adatero.
A Mtalimanja akuti anthu omwe akudzapikisana pa mipando yosiyanasiyana ayenera kudzapereka zikalata zawo kuyambira pa Julaye 24 mpaka 30.