Imfa ya wa kabanza
Anthu okwiya m’taunishipi ya Machinjiri mu mzinda wa Blantyre aphwanya mazenera ndi zitseko za polisi yaing’ono ya Nanthoka ndi kuotcha nyumba ya mkulu wina pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa wa ntchito wake wa njinga ya kabanza.
Khamu lidakhamukira ku Area 7 m’taunishipiyo pa 20 June pomwe apolisi amanyamula thupi la Mphatso Bitoni yemwe adapezeka atabaidwa pa khosi ndipo mpeniwo achiwembu adausiya pakhosi pomwepo.

Malingana ndi mneneri wapolisi m’chigawo ndi kummawa cha kummwera kwa dziko lino Mayi Beatrice Mikuwa, a Aaron Gunda adalemba Bitoni kuti aziwayendetsera njinga yawo koma Lachisanu lapitalo adapezeka ataphedwa ndi anthu osadziwika ndipo njinga yawo idabedwa.
Iwo ati Lachinayi pa 26 June, anthu ena osadziwika adayamba kufalitsa kuti njinga yomwe malemuyo amayendera ili ku nyumba kwa bwana wakeyo zomwe zidapereka chithunzithuzi choti mkuluyo akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa wa ntchito wakeyo.
“Atamva mphekeserayi a Gunda adathamanga kukawafotokozera apolisi ndipo posakhalitsa gulu la anthu oyendetsa njinga za moto lidafika pa polisiyo ndi kupempha kuti akufuna a Gunda powaganizira kuti amadziwa china chake pa imfa ya wa ntchito wawo,” adatero iwo.
A Mikuwa adaonjeza kuti poona kuti apolisi akukana kuchita zomwe gululi limafuna, lidayamba kuotcha polisiyo kenako lidapita ku nyumba ya a Gunda komwe adaba katundu osiyanasiyana kuphatikizapo kuotcha nyumba ya woganiziridwayo.
Apa apolisi adzudzula khalidwe lomwe anthuwa aonetsa ponena kuti akhazikitsa kafukufuku pa nkhaniyi ndipo aliyense yemwe watenga mbali pa zipolowezi lamulo ligwira ntchito.
A Gunda adavulazidwa m’mutu pa ziwawazo ndipo ali ndi zaka 44. Iwo amachokera mudzi wa Chipeta, mfumu yayikulu Chikowi m’boma la Zomba.