Nkhani

Namiwa alira: dzikoli lafika apa?

Patangotha masiku atatu akuluakulu a nthambi za chitetezo atasankha atsogoleri a za chitetezo pomwe dziko lino likukonzekera Chisankho Chachikulu pa 16 September, zigandanga zomwe zidali ndi zida zoopsa zidasasantha a Silvester Namiwa, mmodzi mwa omenyera ufulu Amalawi, amene amakonza zionetsero zoti wapampando wa bungwe la MEC a Annabel Mtalimanja komanso mkulu wa zisankho a Andrew Mpesi atule pansi maudindo awo.

Izi zidachitika pa zionetsero zimene zinkachitika mu mzinda wa Lilongwe ndipo galimoto la mtundu wa Toyota Fortuner lidafika pa bwalo la Lilongwe Community, pomwe a Namiwa amati aziyamba ulendo wokapereka madando awo kwa DC wa Lilongwe, momwe ochita zionetsero adachitira m’madera ena.

Zigandanga zidakwapula a Namiwa ndi zikwapu, zibonga ndi nkhuni. Apolisi akuonera. I Jacob Nankhonya

Zigandangazo zidafika pa malowo pa galimoto la mtundu wa Toyota Fortuner. Zina zinkamveka zikunena kuti: “Kodi uyunso ndiye ndani? Ndi ndani uyu.”

Apo n’kuti a Namiwa akulira chokweza: “Kodi dziko lathuli lafika pamenepa? Apolisi chonde ndithandizeni.”

Komatu apolisiwo palibe chimene adachita, zigandangazo zikukwapula a Namiwa ngati zikupha nkhumba. Malinga ndi zithunzi komanso mavidiyo amene taona, zidagwiritsa ntchito mitengo, matcheni ndi zikwanje pomenya a Namiwa.

Zonsezi zikudza patangotha masiku ochepa mmodzi mwa akuluakulu wa asilikali a Major General Saiford Kalisha, Mayi Yolamu, mkulu wa za ndende a Masauko Ng’ombeyagwada Wiscot komanso wachiwiri kwa mkulu wa za nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko lino atawasankha kukhala akuluakulu amene ‘aonetsetse kuti chisankho cha chaka chino chiyende mwa bata ndi mtendere’.

Potsatira zimene zidachitika ku Lilongweko, akazembe, a mabungwe, zipani zotsutsa ndi ena ambiri anenetsa kuti zidachitikazo n’zosayenera.

Wotsogolera ofesi ya kazembe wa dziko la America Mayi Cameron Diaz adati adachita dambisi ndi nkhanza zidachitikazo. “Zatidetsa kukhosi kuona nkhanza zotere kwa anthu ochita zionetsero mwaufulu. Zatikhudzanso kuti apolisi ndi asilikali a n k h o n d o ad a l e p h e r a kuteteza nzika zinzawo kuti zionetserozo zichitike mosaopa,” adatero iwo.

Ndipo bungwe la oimira anthu pa milandu la Malawi Law Society nalo ladzudzula nkhanzazo ndipo lanenetsa kuti Mayi Yolamu komanso nduna ya chitetezo cha m’dziko a Ezekiel Ching’oma ayenera kutula pansi maudindo awo.

M’chika lata chimene asainira ndi mkulu wa MLS a Davis Njobvu ndi mlembi wa bungwelo a Francis M’mame, iwo ati zimene zidachitikazo zikusonyeza kulephera kwa awiriwo.

“Kumangoonerera anthu akumenyedwa chotero kudzetsa chikaiko chachikulu pa momwe mkulu wa apolisi akugwirira ntchito yawo. Ndipo zimene zachitikazi n’zokwanira kuti a Yolamu atule pansi udindo. Ndipo a C h i n g ’oma o mwe adapatsidwa mphamvu m’gawo 153 ndime 4 ya malamulo aakulu m’dziko lino alephera ntchito yawo yoonetsetsa kuti apolisi akusunga mwambo,” adatero iwo.

Ndipo mkulu wa bungwe la atolankhani la Misa Malawi a Golden Matonga adati mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ayenera kukumbukira lonjezo lawo pamene adakhala ndi olemba nkhani pa mfwisulo wa tsiku lokumbukira olemba nkhaniwa pa 3 May.

“Uf ulu wosonkhana ndi ufulu wokamba za ku k h o s i u may en d er a limodzi. Kulepheretsa anthu kukumana ndi kunena za kukhosi n’kuphwanya ufulu ndipo zisonyeza kulephera,” atero a Matonga.

Mkulu wa zipani zotsutsa boma a George Chaponda, mtsogoleri wa chipani cha UTM komanso mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi ndi ena mwa a ndale amene adzudzula zimene zidachitika ku Lilongwezo.

“ N d i p o a m e n e a k u k h u d z i d w a n d i nkhaniyi amangidwe ndi kuz engedwa mi l andu posokoneza zionetsero za bata zimene nzika za Malawi zimachita. Komanso boma lifotokoze bwino lomwe kuti ufulu wa Amalawi ndi wotetezedwa motani lero ndi kupita mtsogolo,” atero a Chaponda.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button