Nkhani

A Muluzi atseka makomo a mtopola pa ndale

Kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa ati atsogoleri a ndale aphunzirepo pa maganizidwe a mtsogoleri wakale a Bakili Muluzi podzudzula ndale za mtopola zomwe ati zikhoza kuyambitsa chisokonezo mdziko.

A Thindwa ati m’maiko momwe mudabuka nkhondo za pachiweniweni chiyambi chake ndi malankhulidwe osasamala pamisonkhano ya ndale komanso kumema otsatira chipani kuti azichitira mtopola anzawo.

Adayankhula zomanga: A Muluzi

“Tithokoze mtsogoleri wopuma a Muluzi kaamba ka maganizidwe awo ndipo andale ena atengerepo nzeru. Zimakhala ngati zopepuka polankhula koma zimatha kukula kwambiri,” atero a Thindwa.

Mawuwa akutsatira zomwe a Muluzi adanena potsegulira msonkhano waukulu wa chipani cha UDF mu mzinda wa Blantyre Lachitatu pomwe amadzudzula malankhulidwe onyula pa misonkhano.

Izi zikutsatira momwe adalankhula mmodzi mwa aphungu a chipani cha DPP a Daud Chikwanje omwe adauza anthu kumeneko kuti akapeza munthu atavala makaka a chipani cha MCP azimuyatsa moto. Mlanduwo uli kubwalo la milandu koma a Chikwanje adatulutsidwa pabelo Lachinayi.

A Thindwa: Atsogoleri atengepo nzeru

A Muluzi ndi mmodzi mwa Amalawi omwe adamenya nkhondo yofuna ulamuliro wa demokalase m’dziko muno ndipo akhala akuonetsa ntchito zovomereza ndale za demokalase.

M’mawu awo a Muluzi adati akufuna zipani zonse zizimvetsetsana ndi kulolerana pa ndale zawo kuti demokalase yomwe Amalawi ankafuna ioneke.

Ku msonkhano wa UDF kudapita zipani zodziwika kupatula cha MCP chifukwa mamembala ena achipani cha UDF sadagwirizane ndi ganizo loitana chipani cha MCP.

A Muluzi adati zomwe amaganiza mamembala achipaniwo n’zolakwika chifukwa pa demokalase pamafunika kumvana osati mtopola kupewa zolakwika zina.

A Thindwa ati a Muluzi adalankhula mawu omanga ndipo n’zokomera dziko zofunika atsogoleri onse a ndale atengeleko nkumalangiza otsatira zipani zawo.

“Asamatero andalewo chifukwa ndale za demokalase sizifunika mtopola. Malawi ndi dziko la mtendere tsono zimenezo nzosaloledwa,” adatero a Thindwa.

Pano akuluakulu awiri a chipani cha DPP ali mb’walo lamilandu kuyankha mirandu yoyankha malankhulidwe awo pamisankho ya ndale zomwe dziko likudilira kumva zotsatira.

Ku kovenshoniyo, a Atupele Muluzi adatenga mpando wa upulezidenti popanda opikisana nawo monga momwe zipani zonse zomwe zapanga makovenshoni zidayendera.

Nthumwi zidasankha a Raheem Elias ndi Mayi Victoria Mponela kukhala achiwiri kwa a Muluzi pomwe a Genarino Lemani ndi mlembi wamkulu, a Yowoyani Mponela ndi msungichuma pomwe a Dyson Jangiya ndi wofalitsa nkhani.

Omwe anali pulezidenti wa chipanicho mayi Lilian Patel tsopano ndi wapampando wa chipanicho wa dziko lonse.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button