Chichewa

Adona Hilida akadangobwera

Listen to this article

Ngakhale pa Wenela padali zovuta, malo aja timakonda padali kuphulika nyimbo.

Ine nilibe pulobulemu

Nilibe pulobulemu….

Chifukwatu timayembekezera kuti wotisiyayo mtembo wake ufika masana a tsiku limenelo.

Titakhala pamalopo, adabwera mkulu wina akuthamanga.

tadeyo

“Akuluakulu,tiyeni mukandithandize kukhazikitsa mtima pansi bambo a malemu, akufika kumene kuchokera kwawo kwa Govala,” adatero mkulu uja, thukuta lochita kusamba.

Tidakhamukira komweko! Koma mkulu adavuta.

“Mwana wanga Boyisi waferanji? Boyisi anditumizira bulangete kuchoka ku Joni ndani? Ndikuti osandigwira!” adali kulira mkuluyo.

“Pepani, pepani,” wina ankayesera kumutonthoza.

Mkulu adali ndi mavuvu! “Osandigwira! Boyisi waferanji mwana wanga? Bwanji sunandifonere kuti unditsanzike? Osandigwira ineeeeee!”

Anthu okwana 10 adakwanitsa kumukhazika pansi. Adali kufwenthera ndipo ine ndidakhala moyandikana naye.

“Mwamwa kale tiyi?” adandinong’oneza mkuluyo.

Abale anzanga, matchona amayenera kubwera kumudzi akakhalakhala kunjako.

Nkhani idayala nthenje pa Wenela usiku umenewo kusiwa idali ya matchona.

“Koma mtchona wamkulu ndi Adona Hilida! Makhrisimasi awiri ndithu ali mliyenda! Ndalama ali nazo,” adatero Gervazzio.

“Ali ku exile! Anyamata ambiri amakhala ku exile asanalande ulamuliro koma Adona Hilida adathawira kunja ulamuliro utawasempha, ntchito za manja awo poboola mipopi ya chuma zitawachitira umboni,” adatero Abiti Patuma.

“Muli ndi umboni wanji kuti zikuwakhudza? Mudaliko?” adafunsa mkulu amene adali naye tsiku limenelo.

“Mufunanso umboni wotani kuposa zomwe zikuonekeratuzi? Adathawiranji? Nanga anthu onse akuwatchula Adona Hilidawa angakhale kuti akulota?” adayankha Abiti Patuma.

Abale anzanga, inetu zimandisempha.

“Ndipo akadangobwera nthawi ya Khrisimasiyi chifukwatu ndiye chochita sangachisowe. Akhoza kumagulitsa nawo mabaluni ngakhalenso makombola awandawa. Chochita sichingasowe,” adatero Gervazzio.

“Komanso anthu onsewa akuti ndalamazo zidali zakuti Polisi Palibe idzaluzire mpando wonona. Onsewa ngamisala? Akuopa chiyani Adona Hilida? Akadangobwera kuti mlandu wa munda tidzaukambire pamunda pawo pomwepo,” adatero Abiti Patuma.

Kwa ine, ndingothokoza kuti sindili mtchona ngati Adona Hilida. Ndimapuma mpweya mopanda kucheuka! Kusankha n’kwanga kuti ndisangalale Khrisimasi kapena ayi. Pajatu kwathu kwa Kanduku timakhulupirira kuti chisangalalo cha Khrisimasi chidalipo kuyambira kale, Yesu asadabadwe.

Koma izotu sindizitengera kwenikweni pozindikira kuti uzimu ndiwo ufunika.

Sindikulalikira, koma ndi bwino kuthokoza kuti taonanso Khrisimasi ina! Ndi bwino kumayamika Mulungu chifukwa mwamwayi n’kutsetserekera mu 2016. Zaka ndiye zikukhamukira ku 2019 kuti tidzaone Adona Hilida ndi Polisi Palibe akuthotha Moya Pete ndi Dizilo Petulo Palibe.

Gwira bango upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button