Akhazikitsa komiti younika milandu ya zisankho
Mabwalo a milandu asankha komiti younika ndi kuthamangitsa milandu yokhudza zisankho za pa 16 Seputembala.
Mneneri wa makhoti m’dziko muno a Ruth Mputeni akuti wapampando wa komitiyi ndi woweruza wakhoti lalikulu a Dorothy NyaKaunda Kamanga pamene achiwiri awo ndi woweruza ndi a Thomson Ligowe.

Mamembala ena a komitiyi ndi oweruza milandu a Joseph Chigona, Texious Masoamphambe, Violet Chipao, Eddah Ngwira-Mwakibinga, Innocent Nebi, Paul Chiotcha, Wahabi Shaibu ndi a Josephine Masamba.
Ena omwe ali mu komitiyi ndi a Edith Chikagwa, Zikani Msuku ndi a Nellie Mchenga.
“Izi si zikutanthauza kuti komitiyi iziweruza ndi kugamula milandu ya zisankho, koma iziunika ndi kupeza njira zothana mikangano nthawi ya zisankho.
“Ntchito yoweruza milandu idakali m’manja mwa oweruza a makhoti osiyanasiyana,” iwo atero.
Mmbuyomu milandu ya zisankho imachedwa kaamba koti padalibe komiti younika ndi kuthamangitsa milandu ya zisankho.
monga Kenya, Venezuela ndi Phillipines zotsatira zake zidali zosadalirika, koma a Mtalimanja akuti izi ndi nkhambakamwa chabe.
MEC ikuti igwiritsabe ntchito Simatimatiki, koma nazo zipani zotsutsa zatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sizitheka.
Mfumu Mlongoti ya m’dera la Mfumu Chikulamayembe m’boma la Rumphi yati ndi yokondwa ndi kukhazikitsidwa kwa komitiyo chifukwa ithandiza kuti milandu ya zisankho isamatenge nthawi yatali isadagamulidwe.
“Ndiyamikire makhoti kaamba kokhazikitsa komitiyo.
“Mmbuyomu milandu ya zisankho imatenga nthawi yaitali isadagamulidwe,“ iwo adatero.
A Isaac Lomoni, womwe amachita bizinesi mu msika wa Ndirande ku Blantyre, nawonso akuti ndiwokondwa.



